Danieli 11:18 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Kenaka idzatembenukira ku mayiko a mʼmbali mwa nyanja ndi kulanda mizinda yambiri, koma mtsogoleri wina wa nkhondo adzathetsa kudzikuza kwakeko ndipo adzabwezera chipongwecho kwa iye. Onani mutuwoBuku Lopatulika18 Pambuyo pake adzatembenuzira nkhope yake kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwake adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Pambuyo pake adzatembenuzira nkhope yake kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwake adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwake. Onani mutuwo |
“Ndidzayika chizindikiro pakati pawo, ndipo ndidzatumiza ena mwa iwowa amene anapulumuka kuti apite kwa anthu a mitundu ina inu ku Tarisisi, ku Libiya ndi ku Ludi (akatswiri a mauta) ku Tubala ndi Grisi, ndi ku mayiko akutali a mbali mwa nyanja amene sanamvepo za mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga. Iwo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina.