Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 11:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mfumu ya kumpoto idzachita zofuna zake; palibe aliyense adzayigonjetse. Idzakhazikitsa ulamuliro wake mu Dziko Lokongola. Zonse zidzakhala mu ulamuliro wa mfumu yakumpoto ija.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Koma iye amene amdzera kulimbana naye adzachita chifuniro chake cha iye mwini; palibe wakulimbika pamaso pake; ndipo adzaima m'dziko lokometsetsalo, ndi m'dzanja mwake mudzakhala chionongeko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Koma iye amene amdzera kulimbana naye adzachita chifuniro chake cha iye mwini; palibe wakulimbika pamaso pake; ndipo adzaima m'dziko lokometsetsalo, ndi m'dzanja mwake mudzakhala chionongeko.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 11:16
11 Mawu Ofanana  

Ndipo adzalowa mwamphamvu mʼdziko la Yuda, adzasefukira, adzapitirira mpaka kumuyesa mʼkhosi. Mapiko ake otambasuka adzaphimba dziko lako lonse, iwe Imanueli!”


“Ine mwini ndinati, “ ‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana anga ndikukupatsani dziko labwino kwambiri, cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’ Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’ ndi kuti simudzaleka kunditsata.


Kenaka mfumu yamphamvu idzafika imene idzalamulira ndi ufumu waukulu ndi kuchita zimene ifuna.


“Mfumu ya kumpoto idzachita zimene ikufuna. Idzadzikweza ndi kudziyesa yopambana mulungu aliyense ndipo idzanenera za mwano Mulungu wa milungu. Iyo idzapambana mpaka nthawi yoti Mulungu ayilange mwa mkwiyo itakwana popeza chimene chatsimikizika chiyenera kuchitika.


Idzalowanso mʼDziko Lokongola ndipo anthu ambiri adzaphedwa. Koma Edomu, Mowabu ndi olamulira a Amoni adzapulumuka.


Mfumuyo idzayimika matenti ake aufumu, pakati pa nyanja ndi phiri lokongola. Komabe mapeto ake mfumuyo idzaphedwa, ndipo palibe amene adzayithandize.”


Chifukwa cha udindo waukulu umene anapatsidwanso, anthu onse ndi mitundu ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana ankanjenjemera ndikumuopa iye. Amene mfumu inafuna anawaphadi; amene inafuna kuwasunga, inawasunga; amene inafuna kuwakweza, inawakweza; ndipo amene inafuna kuwatsitsa, inawatsitsa.


Ndinaona nkhosa yayimunayo ikuthamanga mwaukali kupita kumadzulo, kumpoto ndi kummwera. Palibe chirombo chimene chikanatha kulimbana nayo, ndipo palibe akanatha kulanditsa kanthu kwa iyo. Iyo inachita monga inafunira ndipo inali ndi mphamvu zambiri.


Inafika pafupi ndipo inalimbana nayo mwaukali nkhosa yayimuna ija nʼkuthyola nyanga zake ziwiri. Nkhosa yayimunayo inalibenso mphamvu zogonjetsera mbuziyo; choncho mbuzi ija inagwetsa nkhosayo pansi nʼkuyipondaponda, ndipo palibe akanatha kulanditsa nkhosayo kwa mbuziyo.


Pa imodzi mwa nyangazo panatuluka nyanga imene inali yocheperapo koma inakula kwambiri kuloza kummwera ndi kummawa ndi kuloza dziko lokongola.


Palibe munthu amene adzatha kukugonjetsa masiku onse a moyo wako. Monga Ine ndinakhalira ndi Mose, chomwechonso ndidzakhala nawe. Sindidzakusiya kapena kukataya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa