Danieli 10:13 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Koma mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya ananditchingira pa masiku 21, kenaka Mikayeli, mmodzi mwa angelo akuluakulu anadza kudzandithandiza chifukwa ndinakhala komweko ndi mafumu a ku Peresiya. Onani mutuwoBuku Lopatulika13 Koma kalonga wa ufumu wa Persiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaele, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Persiya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Koma kalonga wa ufumu wa Persiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaele, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Persiya. Onani mutuwo |
“Pa nthawi imeneyo Mikayeli, mngelo wamkulu amene amateteza anthu a mtundu wako, adzabwera. Imeneyi idzakhala nthawi ya mavuto aakulu omwe sanaonekepo kuyambira pachiyambi cha mitundu ya anthu mpaka nthawi ikudzayo. Komatu pa nthawiyi anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzapezeke lolembedwa mʼbuku adzapulumutsidwa.