Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Afilipi 4:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 4:8
67 Mawu Ofanana  

Pakuti ndasankha iyeyu kuti adzatsogolere ana ake ndi a pa banja lake, kuti asunge mawu a Yehova pochita zoyenera ndi zachilungamo. Choncho Yehova adzachita kwa Abrahamu chimene anamulonjeza iye.”


“Sauli ndi Yonatani, pa moyo wawo anali okondedwa ndi okoma mtima, ndipo pa imfa yawo sanasiyanitsidwe. Iwo anali ndi liwiro loposa ziwombankhanga, anali ndi mphamvu zoposa mkango.


Mulungu wa Israeli anayankhula, Thanthwe la Israeli linati kwa ine: ‘Pamene munthu alamulira anthu mwachilungamo, pamene alamulira moopa Mulungu,


“Mudzateteza osalungama mpaka liti, ndi kukondera anthu oyipa?


Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera.


Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.


Miyeso ndi masikelo achilungamo zimachokera kwa Yehova; miyala yonse yoyesera ya mʼthumba anayipanga ndi Yehova.


Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino; odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.


Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.


“Pali akazi ambiri amene achita zinthu zopambana koma iwe umawaposa onsewa.”


Mupatseni mphotho chifukwa cha zimene iye wachita ndipo ntchito zake zimutamande ku mabwalo.


Milomo yake ndi yosangalatsa kwambiri; munthuyo ndi wokongola kwambiri! Uyu ndiye wachikondi wanga ndi bwenzi langa, inu akazi a ku Yerusalemu.


Njira ya munthu wolungama ndi yosalaza, Inu Wolungamayo, mumasalaza njira ya wolungama.


Anatumiza ophunzira awo kwa Iye pamodzi ndi Aherodia. Anati, “Aphunzitsi, tidziwa kuti ndinu wangwiro ndi kuti mumaphunzitsa mawu a Mulungu monga mwa choonadi. Simutekeseka ndi anthu, popeza simusamala kuti kodi ndi ndani?


chifukwa Herode anaopa Yohane ndipo anamuteteza, podziwa kuti iye anali munthu wolungama ndi woyera mtima. Herode akamamva Yohane, ankathedwa nzeru; komabe amakonda kumumvetsera.


Yesu anawawuza kuti, “Inu ndi amene mumadzilungamitsa nokha pamaso pa anthu, koma Mulungu amadziwa mitima yanu. Zinthu zimene anthu amaziyesa zopambana, ndi zonyansa pamaso pa Mulungu.


Ndipo taonani, mu Yerusalemu munali munthu wotchedwa Simeoni, amene anali wolungama ndi wodzipereka. Iye ankadikira chitonthozo cha Israeli, ndipo Mzimu Woyera anali pa iye.


Ndipo taonani panali munthu wina wotchedwa Yosefe, mmodzi wa gulu loweruza, munthu wabwino ndi wolungama.


Iye amene amayankhula za Iye mwini amatero kuti adzipezere ulemu, koma amene amagwira ntchito kuti amene anamutuma alandire ulemu, ameneyo ndiye munthu woona; mu mtima mwake mulibe chinyengo chilichonse.


Anthuwo anayankha kuti, “Ife tachokera kwa Korneliyo, mkulu woyangʼanira asilikali 100. Iye ndi munthu wolungama ndiponso woopa Mulungu, amene amalemekezedwa ndi Ayuda onse. Mngelo woyera anamuwuza kuti mupite ku nyumba yake kuti akamve mawu amene inu mukanene.”


“Munthu wina dzina lake Hananiya anabwera kudzandiona. Iyeyu anali munthu woopa Mulungu ndi wosunga Malamulo. Ayuda onse okhala kumeneko amamupatsa ulemu waukulu.


Choncho abale, sankhani pakati panu anthu asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi anzeru. Ife tidzawapatsa udindo oyangʼanira.


Tiyeni tikhale moyenera monga nthawi ya masana, osati mʼmagulu amadyerero, achiwerewere ndi kuledzera, mʼmadama ndi zonyansa komanso osati mʼmagawano ndi nsanje.


Pakuti olamulira saopseza amene amachita zabwino koma amene amachita zoyipa. Kodi mukufuna kukhala osaopa olamulira? Tsono chitani zoyenera ndipo adzakuyamikirani.


Nʼchifukwa chake aliyense amene atumikira Khristu mʼnjira iyi akondweretsa Mulungu ndi kuvomerezedwa ndi anthu.


Ayi, Myuda weniweni ndi amene ali Myuda mu mtima mwake, ndipo mdulidwe weniweni ndi wa mtima, wochitika ndi Mzimu, osati ndi malamulo olembedwa. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ayi.


Chomwecho musaweruze nthawi yoweruza isanakwane. Dikirani mpaka Ambuye atabwera. Iye adzaonetsa poyera zimene zabisika mu mdima ndipo adzaonetsa maganizo a mʼmitima ya anthu. Pa nthawi imeneyo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko.


Tsopano tikupemphera kwa Mulungu kuti musadzachite kanthu kena kalikonse kolakwa. Osati chifukwa choti anthu aone kuti ife tapambana mayesowo koma kuti mudzachite zokhoza ngakhale anthu atamationa ngati olephera.


Timatumikira Mulungu ngakhale ena amatinyoza ndi ena amatilemekeza, ena amatinenera chipongwe, enanso amatiyamikira. Ena amatitenga kukhala ngati onena zoona, ndipo enanso amatitenga kukhala ngati onena zabodza.


Ndipo tikumutumiza pamodzi ndi mʼbale amene mipingo yonse yamuyamikira chifukwa cha utumiki wake wa Uthenga Wabwino.


Pakuti tikuyesetsa kuchita zolondola, osati pamaso pa Ambuye pokha komanso pamaso pa anthu.


Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,


Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi.


(pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi).


Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa.


Tsatani chilungamo chokhachokha basi kuti mukhale ndi moyo ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.


Abale anga, ndikupitiriza kunena kuti, kondwani mwa Ambuye! Sizondivuta kuti ndilembenso mawu omwewo, ndipo zimenezi nʼzokuthandizani inuyo.


Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo.


Mukatero akunja adzalemekeza makhalidwe anu a tsiku ndi tsiku, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.


Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima.


Momwemonso, akazi akhale olemekezeka, osasinjirira koma oganiza bwino ndi odalirika pa chilichonse.


Akhale wodziwa kusamala bwino banja lake ndi kulera ana ake bwino, kuti akhale omvera ndi aulemu weniweni.


Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.


Akhale mayi woti amadziwika bwino pa ntchito zake zabwino monga kulera ana, kusamalira alendo, kusambitsa mapazi a anthu a Mulungu, kuthandiza amene ali pa mavuto ndi kudzipereka pa ntchito zonse zabwino.


Amayi achikulire uwatenge ngati amayi ako ndipo amayi achitsikana uwatenge ngati alongo ako, nʼkuyera mtima konse.


Koma akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziretsa, wolungama, woyera mtima ndi wosunga mwambo.


amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.


Phunzitsa amuna achikulire kuti akhale osaledzera, aulemu wawo, odziletsa, okhwima mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkupirira.


Pa zonse iwe mwini ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino. Pa chiphunzitso chako uwonetsa kuona mtima ndi kutsimikiza mtima kwako.


Anthu athu aphunzire kudzipereka pogwira ntchito zabwino, nʼcholinga chakuti athandize zinthu zimene zikufunika msangamsanga. Ndipo asakhale moyo osapindulitsa.


Ndi chikhulupiriro chimenechi makolo athu akale anayamikidwa.


Mutipempherere ifenso. Pakuti tikutsimikiza kuti tili ndi chikumbumtima changwiro ndipo timafuna kuchita zinthu zonse mwaulemu.


Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.


Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima.


Tsopano mwayeretsa mitima yanu pomvera choonadi, kuti muzikondana ndi abale anu, kukondana kwenikweni kochokera pansi pa mtima.


Khalani moyo wabwino pakati pa anthu osapembedza kuti ngakhale atakusinjirirani kuti mumachita zoyipa, iwowo akaona ntchito zanu zabwino, adzalemekeza Mulungu pa tsiku lomwe Iye adzatiyendere.


Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri.


Inu okondedwa, iyi ndi kalata yanga yachiwiri kwa inu. Ine ndalemba makalata onse awiri kuti ndikukumbutseni ndi kukutsitsimutsani ndi cholinga choti muzilingalira moyenera.


Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi.


Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.


Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi.


Ndipo tsopano mwana wanga usaope. Ine ndidzakuchitira chilichonse udzapemphe popeza anzanga onse amʼmudzi muno akudziwa kuti ndiwe mkazi wa khalidwe labwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa