Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Afilipi 4:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Kukhala wosauka ndimakudziŵa, kukhala wolemera ndimakudziŵanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoŵeratu.

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 4:12
15 Mawu Ofanana  

Inu munawapatsa mzimu wanu wabwino kuti uwalangize. Inu simunawamane chakudya cha mana chija, ndipo munawapatsa madzi akumwa.


Yehova anandiyankhula ine mwamphamvu, ndipo anandichenjeza kuti ndisamayende mʼnjira za anthuwa. Iye anati:


Popeza tatembenuka mtima, ndiye tikumva chisoni; popeza tazindikira ndiye tikudziguguda pachifukwa. Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa chifukwa tinachimwa paubwana wathu.’


Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.


Iye anawawuza kuti, “Chifukwa chake mphunzitsi aliyense wa malamulo amene walangizidwa za ufumu wakumwamba ali ngati mwini nyumba amene amatulutsa chuma chatsopano komanso chakale.”


Mwa kufatsa ndi kuleza mtima kwa Khristu, ndikukupemphani, ine Paulo amene anthu ena amati ndimachita manyazi tikaonana maso ndi maso ndi inu, koma wosaopa pamene ndili kutali nanu!


Pakuti ena amati, “Makalata ake ndi awukali ndi amphamvu koma maonekedwe a thupi lake ndi wosagwira mtima ndipo mayankhulidwe ake ndi achabechabe.”


Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala.


Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere?


Ndipo pamene ndinali pakati panu, nditasowa kanthu, sindinalemetse munthu aliyense, pakuti abale ena amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkazisowa. Ndayesetsa kuti ndisakhale cholemetsa kwa inu mʼnjira ina iliyonse, ndipo ndidzapitiriza kutero.


Anamupeza mʼchipululu, ku malo owuma ndi kopanda kanthu. Anamuteteza ndi kumusamalira; anamutchinjiriza ngati mwanadiso wake,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa