Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Afilipi 3:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m'lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m'lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Iye ndi ine tikhale amodzi. Sindiyesanso pandekha kukhala wolungama pakutsata Malamulo, koma ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu, chochilandira pakukhulupirira.

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 3:9
56 Mawu Ofanana  

Chamoyo chilichonse pa dziko lapansi chinawonongedwa, kuyambira munthu, nyama, zokwawa ndi mbalame. Nowa yekha ndiye anatsala pamodzi ndi onse amene anali naye.


“Pamene akuchimwirani, popeza palibe munthu amene sachimwa, ndipo Inu nʼkuwakwiyira ndi kuwapereka kwa mdani, amene adzawatenga ukapolo kupita ku dziko lake, kutali kapena pafupi;


Koma Hezekiya anali ndi mtima wonyada ndipo sanachite molingana ndi kukoma mtima kumene Mulungu anamuonetsera. Choncho mkwiyo wa Yehova unali pa iye ndi pa Yuda ndi Yerusalemu.


Koma pamene nthumwi zotumizidwa ndi atsogoleri a ku Babuloni zinabwera kudzamufunsa za chizindikiro chozizwitsa chimene chinachitika mʼdzikomo, Mulungu anamusiya yekha, kumuyesa kuti adziwe zonse zimene zinali mu mtima mwake.


Onse atembenukira kumbali, onse pamodzi asanduka oyipa; palibe amene amachita zabwino, palibiretu ndi mmodzi yemwe.


Musazenge mlandu mtumiki wanu, pakuti palibe munthu wamoyo amene ndi wolungama pamaso panu.


Ndani angathe kudziwa zolakwa zake? Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.


Palibe munthu wolungama pa dziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha ndipo sachimwa.


Ndikubweretsa pafupi tsiku la chipulumutso changa; sichili kutali. Tsikulo layandikira ndipo sindidzachedwa kukupulumutsani ndi kupereka ulemerero wanga kwa Israeli.


Atatha mazunzo a moyo wake, adzaona kuwala, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzalungamitsa anthu ambiri, popeza adzasenza zolakwa zawo.


Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera, aliyense mwa ife akungodziyendera; ndipo Yehova wamusenzetsa zoyipa zathu zonse.


Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.”


Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumuka ndipo Israeli adzakhala pamtendere. Dzina limene adzamutcha ndi ili: Yehova ndiye Chilungamo Chathu.


Mʼmasiku amenewo Yuda adzapulumuka ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere. Dzina limene mzindawu udzadziwike nalo ndi ili: Yehova Chilungamo Chathu.’


“Zaka 490 zinayikidwa kuti anthu a mtundu wako ndi mzinda wanu woyera aleke zoyipa, asiye tchimo. Iwo adzapereka dipo kupepesera zolakwa zawo. Zikadzatero anthu adzaonetsa moyo wachilungamo nthawi zonse. Izi zidzatsimikiza zimene unaziona mʼmasomphenya zija ndi zimene ananenera aneneri. Malo opatulika adzakhazikitsidwa.


Koma pitani kaphunzireni tanthauzo la mawu awa: ‘Ndimafuna chifundo osati nsembe ayi.’ Pakuti sindinabwere kudzayitana olungama koma ochimwa.”


Pakuti mu Uthenga Wabwino anawulula kuti chilungamo chimachokera kwa Mulungu. Kuyambira pachiyambi mpaka potsiriza ndi chilungamo chobwera mwachikhulupiriro, monga kwalembedwera kuti, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”


Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa.


Perekani moni kwa Androniko ndi Yuniya abale anga amene anali mʼndende pamodzi ndi ine. Iwo amadziwika ndi atumwi, ndipo iwo anali mwa Khristu ine ndisanakhale.


Choncho monga momwe tchimo linkalamulira anthu ndi kubweretsa imfa pa iwo, chomwecho kunali koyenera kuti chisomo chilamulire pobweretsa chilungamo kwa anthu, ndi kuwafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu.


Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa


Pakuti zimene Malamulo sanathe kuzichita, popeza anali ofowoka chifukwa cha khalidwe lathu la uchimo, Mulungu anazichita potumiza Mwana wake mʼchifanizo cha munthu ochimwa kuti akhale nsembe yauchimo. Ndipo Iye anagonjetsa tchimo mʼthupi la munthu,


Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso.


Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.


Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.


tikudziwa kuti munthu salungamitsidwa pochita ntchito za lamulo koma ndi chikhulupiriro mwa Yesu Khristu. Chomwecho, ifenso tinakhulupirira Khristu Yesu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro mwa Khristu ndipo osati pochita ntchito za lamulo, chifukwa palibe amene adzalungamitsidwa pochita ntchito za lamulo.


“Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita kapena sasunga mawu a malamulo awa.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”


Kunena za changu changa, ndinkazunza mpingo. Kunena za chilungamo chopezeka chifukwa chotsata malamulo, ineyo ndinali wopanda cholakwa.


Iye anatipulumutsa ndipo anatiyitanira ku moyo oyera mtima, osati chifukwa cha chilichonse chimene tinachita, koma chifukwa cha chikonzero ndi chisomo chake. Chisomo chimenechi anatipatsa ife mwa Khristu Yesu nthawi isanayambe.


Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera


Mulungu anachita zinthu ziwiri, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusintha ndipo Mulungu sangathe kunama. Choncho Mulungu akutilimbikitsa mtima ife amene tinathawira kwa Iye kuti tichigwiritsitse chiyembekezo chimene tinalandira.


Tonsefe timapunthwa mʼnjira zambiri. Ngati wina salakwa poyankhula, ameneyo ndi munthu wangwiro, wodziwa kuyangʼanira bwino thupi lake lonse.


Ndine Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Kwa anthu amene analandira chikhulupiriro cha mtengowapatali chomwe ifenso tinalandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.


Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa