Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Afilipi 1:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndipo moyo wanu udzakhala odzazidwa ndi chipatso cha chilungamo chimene chimachokera mwa Yesu Khristu. Pakuti zimenezi zidzapereka ulemerero ndi matamando kwa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

11 odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ndipo moyo wanu udzakhala wodzaza ndi zipatso za chilungamo zimene mudzaonetsa mothandizidwa ndi Yesu Khristu, kuti anthu onse alemekeze ndi kutamanda Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 1:11
34 Mawu Ofanana  

Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake ndipo masamba ake safota. Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.


Anatipula nachotsa miyala yonse ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri. Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo. Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino, koma ayi, unabala mphesa zosadya.


Ndipo anthu ako onse adzakhala olungama ndipo dzikolo lidzakhala lawo mpaka muyaya. Iwo ndi mphukira imene Ine ndayidzala, ntchito ya manja anga, kuti aonetse ulemerero wanga.


Monga momwe nthaka imameretsa mbewu ndiponso monga munda umakulitsa mbewu zimene anadzala, momwemonso Ambuye Yehova adzaonetsa chilungamo ndi matamando pamaso pa mitundu yonse ya anthu.


Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni, nkhata ya maluwa yokongola mʼmalo mwa phulusa, ndiwapatse mafuta achikondwerero mʼmalo mwa kulira. Ndiwapatse chovala cha matamando mʼmalo mwa mtima wopsinjika. Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo, yoyidzala Yehova kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.


Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.


Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa.


Iye amadula nthambi iliyonse ya mwa Ine imene sibala chipatso, koma nthambi iliyonse imene imabala chipatso amayisadzira bwino kuti ibale zipatso zambiri.


Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga.


Tsono ine nditamaliza ntchito iyi ndi kutsimikiza kuti alandira chipatsochi, ndidzadzera kwanuko kudzakuchezerani pa ulendo wanga popita ku Spaniya.


Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha.


Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.


Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu.


nʼcholinga chakuti, ife amene tinali oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu, tiyamike ulemerero wake.


Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.


Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite.


(pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi).


Osati ndikufuna mphatso zanu, koma ndikufuna kuti pa zimene muli nazo pawonjezerekepo phindu.


Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mʼnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse yabwino, ndi kukula mʼchidziwitso cha Mulungu.


umene unafika kwa inu. Pa dziko lonse lapansi Uthenga Wabwino ukubereka chipatso ndi kukula monga momwe zakhala zikuchitikira pakati panu kuyambira tsiku limene munawumva ndi kuzindikira chisomo cha Mulungu mu choonadi chonse.


Ife timapempherera zimenezi kuti dzina la Ambuye athu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mulemekezedwe mwa Iyeyo. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.


Anthu athu aphunzire kudzipereka pogwira ntchito zabwino, nʼcholinga chakuti athandize zinthu zimene zikufunika msangamsanga. Ndipo asakhale moyo osapindulitsa.


Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.


Khalani moyo wabwino pakati pa anthu osapembedza kuti ngakhale atakusinjirirani kuti mumachita zoyipa, iwowo akaona ntchito zanu zabwino, adzalemekeza Mulungu pa tsiku lomwe Iye adzatiyendere.


inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.


Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.


Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa