Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




3 Yohane 1:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ine ndinali ndi chimwemwe chachikulu pamene abale ena anafika nʼkundifotokozera za kukhulupirika kwako pa choonadi ndiponso mmene umayendera motsata choonadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Pakuti ndinakondwera kwakukulu, pofika abale ndi kuchita umboni za choonadi chako, monga umayenda m'choonadi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti ndinakondwera kwakukulu, pofika abale ndi kuchita umboni za choonadi chako, monga umayenda m'choonadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ine ndidaakondwa kwambiri pamene abale ena adafika nkumafotokoza za moyo wako m'choona, ndiponso za m'mene umayendera motsata choona.

Onani mutuwo Koperani




3 Yohane 1:3
17 Mawu Ofanana  

Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.


Pa nthawi imeneyo Petro anayimirira pakati pa okhulupirira (gulu la anthu pafupifupi 120).


Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi.


Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.


Mʼmapemphero anga onse opempherera inu, nthawi zonse ndimapemphera ndi chimwemwe


Timakukondani chifukwa cha choonadi chimene chimakhala mwa ife ndipo chidzakhala mwa ife mpaka muyaya.


Ndinakondwera kwambiri nditapeza ana anu ena akuyenda mʼchoonadi, monga Atate anatilamulira.


Tsono ndikabwera ndidzakumbutsa zimene iye amachita. Iye amafalitsa nkhani zabodza zonena ife. Ndipo sakhutira ndi zimenezo, komanso iyeyo amakana kulandira abale. Komanso amaletsa amene akufuna kutero, ndipo amawachotsa mu mpingo.


Wokondedwa, ndimakupempherera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndikuti ukhale bwino mʼthupi mwako, monga momwe ulili moyo wako wauzimu.


Palibe chondikondweretsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akukhala mʼchoonadi.


Wokondedwa, ndiwe wokhulupirika pa zimene ukuchitira abale, ngakhale kuti iwowo ndi alendo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa