Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 8:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Pamenepo Davide anaika maboma mu Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Pamenepo Davide anaika maboma m'Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Pambuyo pake Davide adaika maboma a ankhondo ku Damasiko, m'dziko la Siriya. Choncho Asiriyawo adasanduka otumikira Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye. Motero Chauta adampambanitsa Davideyo kulikonse kumene ankapita.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 8:6
26 Mawu Ofanana  

Mafumu onse amene anali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, iwo anachita mtendere ndi Aisraeli ndipo anakhala pansi pawo. Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni.


Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu.


Tsopano chitani zimenezo! Pakuti Yehova analonjeza Davide kuti, ‘Kudzera mwa mtumiki wanga Davide ndidzapulumutsa anthu anga Aisraeli mʼdzanja la Afilisti ndi kuwachotsa mʼmanja mwa adani awo.’ ”


Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.


Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi.


Iye anayika maboma mʼdera lonse la Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.


Davide anagonjetsanso Amowabu. Iye anawalamula kuti agone pansi mʼmizere itatu pa gulu lililonse ndipo anawayeza ndi chingwe. Pa gulu lililonse ankapha anthu amene anali pa mizere iwiri yoyamba, kusiyapo mzere wachitatu. Kotero Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Davide ndipo ankapereka msonkho.


Davide anatenga zishango zagolide za akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu.


Ndipo Solomoni analamulira mayiko onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika mpaka ku malire a dziko la Igupto. Mayikowa ankabweretsa mphatso ndipo anali pansi pa ulamuliro wa Solomoni moyo wake wonse.


Atamwalira Ahabu, Mowabu anawukira Israeli.


Ntchito zina za Yeroboamu ndi zonse zimene anachita, za kupambana kwake pa nkhondo, za mmene anagonjetsera Damasiko ndi Hamati, imene inali mizinda ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?


Ndipo Yehova anali naye ndipo kulikonse kumene anapita zinthu zinkamuyendera bwino. Iye anagalukira mfumu ya ku Asiriya ndipo sanayitumikirenso.


Tsono Mesa, mfumu ya ku Mowabu ankaweta nkhosa, ndipo iye ankayenera kumapereka kwa mfumu ya ku Israeli chaka ndi chaka ana ankhosa onenepa okwanira 100,000 pamodzi ndi ubweya wankhosa 100,000 zazimuna.


Iye anayika maboma ku Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.


Iye anayika magulu a asilikali mʼmizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, ndipo anamanga maboma mu Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Efereimu imene Asa abambo ake analanda.


Inu Ambuye Wamphamvuzonse, Mpulumutsi wanga wamphamvu, mumateteza mutu wanga tsiku lankhondo.


Kodi si Inu Mulungu, Inu amene mwatikana ife ndipo simutuluka pamodzi ndi magulu athu ankhondo.


Kavalo amamukonzera tsiku la nkhondo, koma ndi Yehova amene amapambanitsa.


Yonatani anakantha mkulu wa ankhondo wa Afilisti ku Geba, ndipo Afilisti anamva kuti Aheberi awukira. Tsono Sauli anawuza amithenga kuti alize lipenga mʼdziko lonse la Israeli.


Tsiku lina Yonatani mwana wa Sauli anawuza mnyamata wake womunyamulira zida zake za nkhondo kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka Afilisti tsidya ilo.” Koma iye sanawuze abambo ake.


Tsono gulu lonse la ankhondo, ndiye kuti iwo amene anali mʼmisasa ndi mʼminda ndiponso iwo amene anali ku kaboma ka ankhondo kaja, onse anagwidwa ndi mantha aakulu. Dzikonso linagwedezeka, choncho anthu anachita mantha koopsa.


Yonatani anawuza mnyamata wake womunyamulira zida uja kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka anthu osachita mdulidwewo. Mwina Yehova adzatigwirira ntchito. Palibe chomuletsa Yehova kutipulumutsa, ngakhale tikhale ambiri kapena ochepa.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa