Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 8:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Ndipo pakufika Aaramu a ku Damasiko kudzathandiza Hadadezere mfumu ya ku Zoba, Davide anakanthako Aaramu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo pakufika Aaramu a ku Damasiko kudzathandiza Hadadezere mfumu ya ku Zoba, Davide anakanthako Aaramu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pamene Asiriya a ku Damasiko adaabwera kudzathandiza Hadadezere, mfumu ya ku Zoba, Davide adapha anthu a ku Siriyawo okwanira 22,000.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 8:5
9 Mawu Ofanana  

Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, anakapeza ankhondo oyenda pansi aganyu okwanira 20,000 kuchokera ku Asiriya wa ku Beti Rehobu ndi Aramu-Zoba, komanso ankhondo 1,000 kwa mfumu Maaka ndiponso ankhondo 22,000 ochokera ku Tobu.


Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.


Mulungu sabweza mkwiyo wake; ngakhale gulu lankhondo la Rahabe linawerama pa mapazi ake.


Aigupto ndi anthu chabe osati Mulungu; akavalo awo ndi nyama chabe osati mizimu. Yehova akangotambasula dzanja lake, amene amapereka chithandizo adzapunthwa, amene amalandira chithandizocho adzagwa; onsewo adzathera limodzi.


pakuti Siriya amadalira Damasiko, ndipo Damasiko amadalira mfumu Rezini basi. Zisanathe zaka 65 Efereimu adzawonongedwa kotheratu, sadzakhalanso mtundu wa anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa