Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 7:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndidakhala nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndidagonjetsa adani ako onse, iweyo ukupenya. Tsono ndidzakumveketsa dzina lako kuti lidzafanefane ndi dzina la anthu otchuka a pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 7:9
23 Mawu Ofanana  

“Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu ndipo ndidzakudalitsa; ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.


Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.


Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo, ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.


Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi; ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.


Nawa mawu otsiriza a Davide: “Mawu a Davide mwana wa Yese, mawu a munthu amene wakwezedwa ndi Wammwambamwamba, munthu wodzozedwa ndi Mulungu wa Yakobo, woyimba nyimbo za Israeli:


Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.


Ndipo Davide anatchuka atabwera kokakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere.


Iye anayika maboma mʼdera lonse la Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.


Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita.


Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi.


Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya, Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.


Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake ndi kukantha otsutsana naye.


Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu, koma wakweza odzichepetsa.


Motero Yehova anali ndi Yoswa, ndipo mbiri yake inafalikira dziko lonse.


Davide ankapambana kwambiri pa chilichonse chimene amachita chifukwa Yehova anali naye.


Nthawi zonse pamene atsogoleri a Afilisti ankatuluka kukamenya nkhondo, Davide ankapambana kuposa nduna zonse za Sauli. Choncho dzina lake linatchuka kwambiri.


Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi, ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala. Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu, amawapatsa mpando waulemu. “Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova, anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.


Motero Sauli ndi ana ake atatu, wonyamula zida zake pamodzi ndi anthu ake onse anafera limodzi pa tsikulo.


Choncho anatumiza Bokosi la Mulungu ku Ekroni. Koma Bokosi la Mulungu lija litangofika ku Ekroni, anthu a ku Ekroni analira kuti, “Abwera nalo Bokosi la Mulungu wa Israeli kwa ife kuti atiphe pamodzi ndi anthu athu.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa