2 Samueli 7:22 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Inu ndinu wamkulu, Yehova Wamphamvuzonse! Palibe wina wofanana nanu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha, monga tamvera ndi makutu athu. Onani mutuwoBuku Lopatulika22 Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, palibe Mulungu winanso koma Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 “Zoonadi, ndinu aakulu, Inu Chauta Wamphamvuzonse. Malinga ndi zimene tidamva ndi makutu athu, palibenso wina aliyense wonga Inu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha. Onani mutuwo |
Limeneli ndilo tanthauzo la masomphenya a mwala umene unagamuka pa phiri, koma osati ndi manja a anthu; mwala umene unaphwanya chitsulo, mkuwa, dongo, siliva ndi golide mʼtizidutswa. “Mulungu wamkulu wakuonetsani mfumu chimene chidzachitika kutsogolo. Malotowo ndi woona ndipo tanthauzo lake ndi lodalirika.”