Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 7:14 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Akadzachita choyipa, Ineyo ndidzamulanga ndi ndodo ndi zikwapu za anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

14 Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Akamadzandichimwira, ndizidzamulanga monga m'mene bambo amalangira ana ake.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 7:14
19 Mawu Ofanana  

“ ‘Koma sindidzalanda ufumu wonse mʼdzanja la Solomoni. Ine ndamuyika kukhala wolamulira masiku onse a moyo wake chifukwa cha mtumiki wanga Davide, amene ndinamusankha ndiponso amene anamvera malamulo anga ndi mawu anga.


“Koma ngati iwe kapena ana ako mudzapatuka ndi kuleka kusunga malamulo ndi mawu anga amene ndakupatsani ndi kupita kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza,


Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Ine sindidzasiya kumukonda monga ndinachitira ndi amene unalowa mʼmalo mwawo.


Iye ndiye adzandimangire nyumba. Adzakhala mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake. Ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake waufumu mʼdziko la Israeli mpaka muyaya.’ ”


Yehova anati kwa ine, “Solomoni mwana wako ndiye amene adzamanga nyumba yanga ndi mabwalo anga, pakuti Ine ndamusankha kuti akhale mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake.


“Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula; nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse.


Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula: Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga; lero Ine ndakhala Atate ako.


Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani,’ akutero Yehova. ‘Ngakhale ndidzawononga kotheratu mitundu yonse ya anthu kumene ndinakubalalitsirani, koma inu sindidzakuwonongani kotheratu. Sindidzakulekani kuti mukhale osalangidwa. Koma ndidzakulangani mwachilungamo.’ ”


Ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba kuti, “Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa amene ndikondwera naye.”


Pamene tiweruzidwa ndi Ambuye, ndiye kuti akukonza khalidwe lathu kupewa kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi anthu osakhulupirira.


Ndipo “Ndidzakhala Atate anu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi, akutero Ambuye, Wamphamvuzonse.”


Tsono dziwani mu mtima mwanu kuti monga abambo amalanga mwana wawo, momwemonso Yehova Mulungu wanu amakulangani.


Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati, “Iwe ndiwe mwana wanga; Ine lero ndakhala Atate ako.” Kapena kunenanso kuti, “Ine ndidzakhala abambo ake; iye adzakhala mwana wanga.”


Iye amene adzapambane adzalandira zonsezi, ndipo ndidzakhala Mulungu wake ndi Iye adzakhala mwana wanga.


Amene ndimawakonda ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho chita changu ndipo lapa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa