2 Samueli 7:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzakupatsaninso mpumulo kwa adani anu onse. “ ‘Yehova akulengeza kwa iwe kuti Iye mwini adzakhazikitsa banja lako: Onani mutuwoBuku Lopatulika11 monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israele; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israele; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 kuyambira nthaŵi imene ndidaaika aweruzi a anthu anga Aisraele. Choncho ndidakupumitsa kwa adani ako onse. Kuwonjezera pamenepo, Chauta akukuuza kuti, Ine Chauta ndidzakhazikitsa banja lako. Onani mutuwo |
Ngati udzamvera zonse zimene ndidzakulamula ndi kuyenda mʼnjira yanga ndi kuchita zabwino pamaso panga, posunga malamulo anga ndi mawu anga monga anachitira Davide mtumiki wanga, Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakupatsa ufumu umene udzakhala wokhazikika monga ndinamupatsira Davide, ndipo Ine ndidzakupatsa Israeli.