2 Samueli 6:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Yehova poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga. Onani mutuwoBuku Lopatulika5 Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira za mitundumitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi maseche, ndi nsanje. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira za mitundumitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi maseche, ndi nsanje. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Tsono Davide pamodzi ndi Aisraele onse ankakondwerera kwambiri kulemekeza Chauta poimba ndi mphamvu zao zonse nyimbo ndi azeze, apangwe, tizing'wenyeng'wenye, maseche ndi ziwaya zamalipenga. Onani mutuwo |
Tsopano ngati muli okonzeka kulambira ndi kupembedza fano ndinalipanga, mukangomva kulira kwa lipenga chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muchita bwino. Koma ngati simulipembedza, mudzaponyedwa mʼnganjo ya moto. Nanga ndi mulungu uti amene adzatha kukupulumutsani mʼmanja anga?”