2 Samueli 5:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Tsono Davide anakhazikika mu lingamo ndipo mzindawu anawutcha, Mzinda wa Davide. Iye anamanga malo onse ozungulira kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. Onani mutuwoBuku Lopatulika9 Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mzinda wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mudzi wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Tsono Davide adakhala mu mzinda wamalinga uja nautchula dzina lakuti, “Mzinda wa Davide.” Ndipo adamanga mzinda kuzungulira deralo kuyambira ku malo komwe kale kunali chidikha, kuvuma kwa phiri mpaka m'kati mwake. Onani mutuwo |
Chipata cha Kasupe chinakonzedwa ndi Saluni mwana wa Koli-Hoze, wolamulira chigawo cha Mizipa. Iye anachimanganso ndi kuyikanso denga ndiponso zitseko, zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iye anakonzanso khoma la Dziwe la Siloamu limene lili pafupi ndi munda wa mfumu mpaka ku makwerero otsikira potuluka mzinda wa Davide.