Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 5:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Analamulira Yuda ali ku Hebroni kwa zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi, ndipo ali ku Yerusalemu analamulira Israeli yense ndi Yuda kwa zaka 33.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Ku Hebroni anachita ufumu pa Yuda zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi; ndi ku Yerusalemu anachita ufumu pa Aisraele onse ndi Ayuda omwe zaka makumi atatu mphambu zitatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ku Hebroni anachita ufumu pa Yuda zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi; ndi ku Yerusalemu anachita ufumu pa Aisraele onse ndi Ayuda omwe zaka makumi atatu mphambu zitatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ku Hebroni adalamulira Ayuda zaka zisanu ndi ziŵiri ndi theka. Ndipo ku Yerusalemu adalamulira Israele yense ndi Yuda zaka 33.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 5:5
7 Mawu Ofanana  

Ndinakupatsanso banja la mbuye wako ndiponso akazi a mbuye wako mʼmanja mwako. Ine ndinakupatsanso banja la Israeli ndi Yuda. Ndipo ngati zinthu zonse izi zinali zochepa, Ine ndikanakupatsa zambiri.


Davide anakhala mfumu ku Hebroni akulamulira fuko la Yuda, kwa zaka zisanu ndi chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi.


Kenaka amuna a ku Yuda anabwera ku Hebroni ndipo kumeneko anadzoza Davide kukhala mfumu ya fuko la Yuda. Davide atawuzidwa kuti anthu a ku Yabesi Giliyadi ndi amene anayika mʼmanda Sauli,


Iyeyo nʼkuti atalamulira Israeli kwa zaka makumi anayi. Ku Hebroni analamulira zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33.


Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, iye anachita nawo pangano pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli, monga momwe Yehova analonjezera kudzera mwa Samueli.


Iye analamulira Israeli kwa zaka makumi anayi; zaka zisanu ndi ziwiri ali ku Hebroni ndi zaka 33 ali ku Yerusalemu.


Ana asanu ndi mmodzi awa a Davide anabadwira ku Hebroni kumene analamulirako zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi. Davide analamuliranso mu Yerusalemu kwa zaka 33,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa