Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 5:18 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ndipo Afilisti anabwera ndi kukhala momwazika mʼChigwa cha Refaimu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

18 Tsono Afilisti anafika natanda m'chigwa cha Refaimu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Tsono Afilisti anafika natanda m'chigwa cha Refaimu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Tsono Afilisti adabwera nakhala momwazikana m'chigwa cha Refaimu.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 5:18
8 Mawu Ofanana  

Mʼchaka cha khumi ndi chinayi, Kedorilaomere mogwirizana ndi mafumu ena aja anapita kukagonjetsa Arefaiwa ku Asiteroti-karanaimu, Zuzimu wa ku Hamu, Aemi wa ku Savekiriataimu


Pa nthawi yokolola, atatu mwa atsogoleri makumi atatu anabwera kwa Davide ku phanga la Adulamu, pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu.


Nthawi inanso Afilisti anabweranso namwazikana mʼChigwa cha Refaimu;


Atatu mwa atsogoleri makumi atatu aja anabwera kwa Davide ku thanthwe ku phanga la Adulamu pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu.


Israeli adzakhala ngati munda wa tirigu umene anatsiriza kukolola. Adzakhalanso ngati munda wa mʼchigwa cha Refaimu anthu atatha kukunkha ngala za tirigu.


Ndipo anapitirira mpaka ku chigwa cha Hinomu mbali ya kummwera kwa mzinda wa Ayebusi (mzinda wa Yerusalemu). Kuchokera kumeneko anakwera mpaka pamwamba pa phiri kumadzulo kwa chigwa cha Hinomu cha kumpoto kwenikweni kwa chigwa cha Refaimu.


Yoswa anayankha kuti, “Ngati muli ambiri ndipo dziko la ku mapiri la Efereimu lakucheperani kwambiri, lowani ku nkhalango mudule mitengo, mudzikonzere malo akuti mukhalemo, mʼdziko la Aperezi ndi Arefai.”


Malire anatsikira mʼmphepete mwa phiri loyangʼanana ndi chigwa cha Beni Hinomu, kumpoto kwa chigwa cha Refaimu. Anapitirira kutsikira ku chigwa cha Hinomu kummwera kwa chitunda cha Ayebusi mpaka ku Eni Rogeli.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa