Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 4:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iwo analowa mʼnyumbamo iye akugona pa bedi mʼchipinda chake. Atamulasa ndi kumupha, anadula mutu wake nʼkuwutenga, nayenda usiku wonse mʼnjira yopita ku Araba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Koma polowa iwo m'nyumbamo iye ali chigonere pakama pake m'chipindamo, anamkantha, namupha namdula mutu wake, nautenga namuka njira ya kuchidikha usiku wonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Koma polowa iwo m'nyumbamo iye ali chigonere pakama pake m'chipindamo, anamkantha, namupha namdula mutu wake, nautenga namuka njira ya kuchidikha usiku wonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Aŵiriwo ataloŵa m'nyumbamo, adampeza Isibosetiyo ali gone pabedi pake. Iwo aja adambaya nkumupha, namdula mutu. Adanyamula mutuwo, nayenda nawo usiku wonse kudzera njira ya ku Araba.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 4:7
8 Mawu Ofanana  

Usiku wonsewo Abineri ndi ankhondo ake anayenda kudutsa Araba. Iwo anawoloka Yorodani, napitirira mpaka kudutsa dera lonse la Bitironi ndipo anafika ku Mahanaimu.


Mtsinje wa Nailo udzadzaza ndi achule. Achulewo adzatuluka ndi kukalowa mʼnyumba yaufumu, ku chipinda chogona ndi pa bedi lako, mʼnyumba za nduna zako ndi pa anthu ako ndi mophikira buledi ndiponso mopangira bulediyo.


Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake.


Davide anathamanga nakayimirira pamwamba pa Mfilisiti uja. Anasolola lupanga lake lomwe moyikamo mwake, namupha pomudula mutu wake. Afilisti ataona kuti ngwazi yawo yafa, anathawa.


Pambuyo pake Davide anatenga mutu wa Mfilisitiyo napita nawo ku Yerusalemu, koma anayika zida za Mfilisitiyo mu tenti yake.


Iwo anadula mutu wake ndi kumuvula zida zake zankhondo. Ndipo anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Afilisti kukafalitsa nkhani yabwinoyi kwa mafano awo ndi kwa anthu awo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa