Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 3:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Koma mwamuna wake anapita naye akulira pambuyo pake njira yonse mpaka ku Bahurimu. Kenaka Abineri anati kwa iye, “Bwerera kwanu!” Ndipo anabwerera kwawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Ndipo mwamuna wakeyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Bahurimu. Pomwepo Abinere ananena naye, Choka, bwerera; ndipo anabwerera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo mwamuna wakeyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Bahurimu. Pomwepo Abinere ananena naye, Choka, bwerera; ndipo anabwerera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Koma mwamuna wakeyo adamtsatira mkaziyo. Mwamunayo ankapita nalira njira yonse mpaka ku Bahurimu. Abinere adamuuza kuti, “Iwe, bwerera.” Iye uja nkubwereradi.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 3:16
9 Mawu Ofanana  

Mfumu Davide itayandikira Bahurimu, munthu wochokera ku fuko limodzi ndi banja la Sauli anabwera kuchokera mʼmenemo. Dzina lake linali Simei, mwana wa Gera ndipo amatukwana pamene amabwera.


Koma mnyamata wina anawaona ndipo anakawuza Abisalomu. Kotero anthu awiriwo anachoka mofulumira ndipo anapita ku nyumba ya munthu wina ku Bahurimu. Iye anali ndi chitsime ku mpanda kwake ndipo iwo analowamo.


Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, anabwera mofulumira pamodzi ndi Ayuda kudzakumana ndi mfumu Davide.


Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a fuko la Benjamini pamodzi ndi Ziba, wantchito wa banja la Sauli ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndi antchito ake makumi awiri. Iwo anathamangira ku Yorodani kumene kunali mfumu.


Abi-Aliboni Mwaribati, Azimaveti Mbarihumi,


Kotero Isi-Boseti analamulira ndipo anakamutenga kwa mwamuna wake Palitieli mwana wa Laisi.


“Ndipo kumbukira kuti uli ndi Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wochokera ku Bahurimu, amene ananditemberera koopsa tsiku limene ndimapita ku Mahanaimu. Atabwera kudzakumana nane ku Yorodani, ine ndinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Sindidzakupha iwe ndi lupanga.’


Ismaeli mwana wa Netaniya anachoka ku Mizipa akulira kupita kukakumana nawo. Atakumana nawo, iye anati, “Bwerani mudzaonane ndi Gedaliya mwana wa Ahikamu.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa