Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 24:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Koma Yowabu anayankha mfumu kuti, “Yehova Mulungu wanu achulukitse ankhondo anu kukhala miyandamiyanda, ndipo alole inu mbuye wanga mfumu mudzazione zimenezi. Koma nʼchifukwa chiyani inu mbuye wanga mfumu mukufuna kuchita zimenezi?”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo Yowabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwachulukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu achione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi chinthu ichi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Yowabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwachulukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu achione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi chinthu ichi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma Yowabu adauza mfumu kuti, “Chauta Mulungu wanu achulukitse anthu makumi khumi kupambana m'mene alirimu, ndipo alole kuti inu mbuyanga mfumu mudzaziwone zimenezo. Koma chifukwa chiyani inu mbuyanga mfumu mukufuna chinthu chotere?”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 24:3
7 Mawu Ofanana  

Limba mtima ndipo timenyane nawo mopanda mantha chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu. Yehova achite chomukomera pamaso pake.”


Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu ndi atsogoleri a ankhondo. Choncho anachoka pamaso pa mfumu kupita kukawerenga anthu omenya nkhondo mu Israeli.


Yehova akuwonjezereni madalitso; inuyo pamodzi ndi ana anu.


Gulu lalikulu la anthu ndiye ulemerero wa mfumu, koma popanda anthu kalonga amawonongeka.


Ukadzaona zimenezi udzasangalala kwambiri, mtima wako udzalumpha ndi kudzaza ndi chimwemwe; chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe chuma cha mitundu ya anthu chidzabwera kwa iwe.


Yehova Mulungu wa makolo anu wachulukitsa chiwerengero chanu ndipo wakudalitsani monga momwe analonjezera!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa