Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 23:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi. Monga mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu a Davide, iye anali ndi Davide pamene anazunza Afilisti amene anasonkhana ku Pasi-Damimu kuchita nkhondo. Kenaka ankhondo a Israeli anabwerera mʼmbuyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Mnzake wotsatana naye mwa anthu atatu amphamvu aja anali Eleazara, mwana wa Dodo, mwana wa Aho. Iyeyo anali pamodzi ndi Davide pamene ankaputa Afilisti omwe adaasonkhana kuti amenyane naye nkhondo ku Pasi-Damimu. Aisraele anali atathaŵa.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 23:9
12 Mawu Ofanana  

Amene amalamulira gulu lachiwiri pa mwezi wachiwiri anali Dodai Mwahohi; Mikiloti ndiye anali mtsogoleri wa gulu lake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.


Abisuwa, Naamani, Ahowa,


Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa, koma anthu awiri akhoza kudziteteza. Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.


“Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa, palibe ndi mmodzi yemwe anali nane. Ndinawapondereza ndili wokwiya ndipo ndinawapondereza ndili ndi ukali; magazi awo anadothera pa zovala zanga, ndipo zovala zanga zonse zinathimbirira.


Ndinayangʼana ndipo panalibe munthu wondithandiza. Ndinadabwa kwambiri kuti panalibe wondichirikiza; choncho ndinapambana ndi mphamvu zanga, ndipo mkwiyo wanga unandilimbitsa.


Pamenepo ophunzira ake onse anathawa namusiya yekha.


Ndipo Mfilisitiyo anati, “Bwerani lero timenyane basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.”


Davide anafunsa anthu amene anayima pafupi naye kuti, “Kodi adzamuchita chiyani munthu amene adzapha Mfilisiti uyu ndi kuchotsa chitonzo pakati pa Israeli? Mfilisiti wosachita mdulidweyu ndi ndani kuti azinyoza gulu lankhondo la Mulungu wamoyo?”


Ine kapolo wanu ndinapha mkango ngakhalenso chimbalangondo. Tsono Mfilisiti wosachita mdulidweyu adzaphedwa monga zinazo chifukwa wanyoza ankhondo a Mulungu wamoyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa