Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 23:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 amakhala ngati kuwala kwa mmamawa, mmawa wopanda mitambo, monga kuwala pamene mvula yaleka kugwa imene imameretsa udzu mʼnthaka.’

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa, potuluka dzuwa, M'mawa mopanda mitambo; pamene msipu uphuka kutuluka pansi, chifukwa cha kuwala koyera, italeka mvula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa, potuluka dzuwa, M'mawa mopanda mitambo; pamene msipu uphuka kutuluka pansi, chifukwa cha kuwala koyera, italeka mvula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 amaŵafikira ngati kuŵala kwam'maŵa amaŵaŵalira ngati dzuŵa lam'maŵa pa tsiku lamitambo. Alinso ngati mvula imene imameretsa udzu pa nthaka.’

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 23:4
17 Mawu Ofanana  

Ankhondo ako adzakhala odzipereka pa tsiku lako la nkhondo. Atavala chiyero chaulemerero, kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha, udzalandira mame a unyamata wako.


Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.


kuti zidzukulu zake zidzakhale kwamuyaya ndipo mpando wake waufumu udzakhazikika pamaso panga ngati dzuwa;


Koma njira ya anthu olungama ili ngati kuwala kwa mʼbandakucha kumene kumanka kuwalirawalira mpaka dzuwa litafika pa mutu.


Pakuti Yehova akunena kwa ine kuti, “Ndili chikhalire ku malo anga kuno, ndidzakhala chete, ndi kumangoyangʼana, monga momwe dzuwa limawalira nthawi yotentha, monganso momwe mame amagwera usiku pa nthawi yotentha yokolola.”


Tsiku limenelo Nthambi ya Yehova idzakhala yokongola ndi yaulemerero, ndipo chipatso cha mʼdziko chidzakhala chonyaditsa ndi chopereka ulemerero kwa onse opulumuka mu Israeli.


“Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika, ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira.


Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwako ndipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako.


Tiyeni timudziwe Yehova, tiyeni tilimbike kumudziwa Iye. Adzabwera kwa ife mosakayikira konse ngati kutuluka kwa dzuwa; adzabwera kwa ife ngati mvula ya mʼchilimwe, ngati mvula ya nthawi yamphukira imene imakhathamiritsa nthaka.”


Choncho ndakuwazani ngati nkhuni kudzera mwa aneneri anga, ndakuphani ndi mawu a pakamwa panga; chigamulo changa chinangʼanima ngati mphenzi pa inu.


Otsalira a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu ngati mame ochokera kwa Yehova, ngati mvumbi pa udzu, omwe sulamulidwa ndi munthu kapena kudikira lamulo la anthu.


Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola.


Iye anabwera ngati mboni kudzachitira umboni kuwunikako kuti kudzera mwa iye anthu onse akhulupirire.


Chiphunzitso changa chigwe ngati mvula ndipo mawu anga atsike ngati mame, ngati mvumbi pa udzu watsopano, ngati mvula yochuluka pa zomera zanthete.


“Choncho Yehova! adani anu onse awonongeke, koma iwo amene amakukondani inu akhale ngati dzuwa pamene lituluka ndi mphamvu zake.” Ndipo dziko linakhala pa mtendere zaka makumi anayi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa