2 Samueli 20:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Davide anati kwa Abisai, “Tsono Seba mwana wa Bikiri adzatipweteka kuposa momwe Abisalomu anatichitira. Tenga asilikali a mbuye wako ndipo umuthamangitse, mwina adzapeza mizinda yotetezedwa ndi kutithawa ife.” Onani mutuwoBuku Lopatulika6 Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Sheba mwana wa Bikiri adzatichitira choipa choposa chija cha Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze mizinda ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Sheba mwana wa Bikiri adzatichitira choipa choposa chija cha Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze midzi ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Pamenepo Davide adauza Abisai kuti, “Sheba, mwana wa Bikiri, adzativuta kwambiri kupambana Abisalomu. Tenga ankhondo anga mulondole Shebayo kuti angadzipezere mizinda yamalinga namativutitsa.” Onani mutuwo |
Uriya anayankha Davide kuti, “Bokosi la Chipangano ndi Israeli ndiponso Yuda akukhala mʼmatenti, ndipo mbuye wanga Yowabu ndi ankhondo anu mbuye wanga amanga misasa pa mtetete. Ine ndingapite bwanji ku nyumba yanga kukadya ndi kumwa ndiponso kugona ndi mkazi wanga? Pali inu wamoyo, ine sindidzachita chinthu chimenechi.”