Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 20:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Davide atabwerera ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, iye anatenga azikazi khumi aja amene anawasiya kuti aziyangʼanira nyumba yaufumu, ndipo anawayika mʼnyumba imene anayikapo mlonda. Iye ankawadyetsa koma sanagone nawonso. Anasungidwa kwa okha mpaka tsiku la kufa kwawo ndipo anakhala ngati akazi amasiye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo Davide anafika kunyumba kwake ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi aang'onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m'nyumba, nawapatsa chakudya, koma sanalowane nao. Chomwecho iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Davide anafika kunyumba kwake ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi ang'onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m'nyumba, nawapatsa chakudya, koma sanalowane nao. Chomwecho iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Davide atafika ku nyumba yake ku Yerusalemu, adatenga azikazi ake khumi amene adaaŵasiya kuti azisunga mudzi, naŵatsekera m'nyumba m'mene adaaikamo mlonda woŵalonda. Ankaŵapatsa chakudya, koma Davide sankaloŵa m'nyumbamo kwa akaziwo. Adaŵatsekera m'nyumba choncho mpaka tsiku la kufa kwao, ndipo ankakhala ngati akazi amasiye.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 20:3
4 Mawu Ofanana  

ndipo anakawatsekera mʼndende, nakawayika mʼmanja mwa mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa mfumu kuja, mʼndende momwe Yosefe ankasungidwamo.


Mfumu inanyamuka pamodzi ndi banja lake lonse. Koma iye anasiya azikazi khumi kuti azisamalira nyumba yaufumu.


Kotero Aisraeli onse anamuthawa Davide ndipo anatsatira Seba mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda anakhala ndi mfumu yawo njira yonse kuchokera ku Yorodani mpaka ku Yerusalemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa