2 Samueli 20:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Kotero Aisraeli onse anamuthawa Davide ndipo anatsatira Seba mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda anakhala ndi mfumu yawo njira yonse kuchokera ku Yorodani mpaka ku Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Lopatulika2 Chomwecho anthu onse a Israele analeka kutsata Davide, natsata Sheba mwana wa Bikiri; koma anthu a Yuda anaphatikizana ndi mfumu yao, kuyambira ku Yordani kufikira ku Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Chomwecho anthu onse a Israele analeka kutsata Davide, natsata Sheba mwana wa Bikiri; koma anthu a Yuda anaphatikizana ndi mfumu yao, kuyambira ku Yordani kufikira ku Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Choncho Aisraele onse adaleka kumtsata Davide, nayamba kutsata Sheba, mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda adakhalabe nganganga pambuyo pa mfumu yao, kuyambira ku Yordani mpaka ku Yerusalemu. Onani mutuwo |
Davide atabwerera ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, iye anatenga azikazi khumi aja amene anawasiya kuti aziyangʼanira nyumba yaufumu, ndipo anawayika mʼnyumba imene anayikapo mlonda. Iye ankawadyetsa koma sanagone nawonso. Anasungidwa kwa okha mpaka tsiku la kufa kwawo ndipo anakhala ngati akazi amasiye.