Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 2:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pa nthawi imeneyi Abineri mwana wa Neri, wolamulira ankhondo a Sauli, anatenga Isi-Boseti mwana wa Sauli ndi kubwera naye ku Mahanaimu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Abinere mwana wa Nere, amene ankalamula ankhondo a Saulo, anali atatenga Isiboseti mwana wa Saulo, kupita naye kutsidya, ku Mahanaimu.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 2:8
18 Mawu Ofanana  

Pamene Yakobo anawaona anati, “Ili ndi gulu la Mulungu.” Choncho anawatcha malowo Mahanaimu.


Yakobo anatumiza amithenga ake kwa mʼbale wake Esau ku dera la Seiri, dziko la Edomu.


Davide anapita ku Mahanaimu, ndipo Abisalomu anawoloka Yorodani pamodzi ndi ankhondo ena onse a Israeli.


Usiku wonsewo Abineri ndi ankhondo ake anayenda kudutsa Araba. Iwo anawoloka Yorodani, napitirira mpaka kudutsa dera lonse la Bitironi ndipo anafika ku Mahanaimu.


Tsopano khalani amphamvu ndi olimba mtima, pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndipo fuko la Yuda landidzoza kukhala mfumu yawo.”


Ndipo mfumu inati kwa ankhondo ake, “Kodi inu simukudziwa kuti lero mu Israeli mwagwa kalonga ndi munthu wamkulu?


Pamene kunali nkhondo pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide, Abineri anayamba kudzipatsa yekha mphamvu pakati pa banja la Sauli.


Anthu a fuko la Benjamini, abale ake a Sauli analipo 3,000 ndipo ambiri anali ndi Sauli ku nyumba yake pa nthawiyi;


Anthu a fuko la Efereimu, asilikali olimba mtima, otchuka pa mabanja awo analipo 20,800;


Neri anabereka Kisi. Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala.


Neri anabereka Kisi, Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala.


Kuchokera ku fuko la Gadi analandira mzinda wa Ramoti ku Giliyadi. Mzinda umene unali wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi.


Dzina la mkazi wake linali Ahinoamu. Iyeyu anali mwana wa Ahimaazi. Dzina la mkulu wa ankhondo a Sauli linali Abineri mwana wa Neri, mʼbale wa abambo a Sauli.


Sauli ataona Davide akupita kukakumana ndi Mfilisitiyo anafunsa Abineri, mkulu wa ankhondo kuti, “Abineri, kodi mnyamatayu ndi mwana wa yani?” Abineri anayankha kuti, “Ndithu mfumu muli apa ine sindikumudziwa.”


Davide anayitana gulu lankhondo ndi Abineri mwana wa Neri nawafunsa kuti, “Kodi sundiyankha ine Abineri?” Abineri anayankha kuti, “Ndiwe yani amene ukuyitana mfumu?”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa