Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 2:32 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Iwo anatenga Asaheli ndi kukamuyika mʼmanda a abambo ake ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi ankhondo ake anayenda usiku wonse ndi kufika ku Hebroni kukucha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

32 Ndipo ananyamula Asahele namuika m'manda a atate wake ali ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi anthu ake anachezera kuyenda usiku wonse, ndipo kudawachera ku Hebroni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo ananyamula Asahele namuika m'manda a atate wake ali ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi anthu ake anachezera kuyenda usiku wonse, ndipo kudawachera ku Hebroni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Tsono adatenga mtembo wa Asahele, nakauika m'manda a bambo wake, amene anali ku Betelehemu. Yowabu ndi anthu ake adayenda usiku wonse, ndipo kudaŵachera ali ku Hebroni.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 2:32
10 Mawu Ofanana  

Nthawi itayandikira yoti Israeli amwalire, anayitanitsa mwana wake Yosefe nati kwa iye, “Ngati ukundikondadi monga abambo ako, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga ndipo ulonjeze kuti udzaonetsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwako kwa ine kuti sudzayika mtembo wanga kuno ku Igupto.


Ine ndikagona pamodzi ndi makolo anga. Choncho ndikadzamwalira udzanditulutse mu Igupto muno ndipo ukayike mtembo wanga kumene anayikidwa makolo anga.” Yosefe anati, “Ndidzachita monga mwanenera.”


Koma ankhondo a Davide anapha ankhondo a fuko la Benjamini 360 amene anali ndi Abineri.


Mafuko onse a Israeli anabwera kwa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife mafupa ndi mnofu wanu.


Iye anayikidwa mʼmanda amene anadzisemera yekha mu Mzinda wa Davide. Anagoneka mtembo wake pa chithatha chimene anayikapo zonunkhira zamitundumitundu, ndipo anasonkha chimoto chachikulu pomuchitira ulemu.


Yehosafati anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Ndipo Yehoramu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.


Kodi ukumuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzatumikira mafumu; sadzatumikira anthu wamba.


Gideoni mwana wa Yowasi anamwalira atakalamba ndipo anayikidwa mʼmanda a abambo ake, Yowasi ku Ofura mzinda wa Mwabiezeri.


Sauli anamufunsa, “Mnyamata iwe, kodi paja ndiwe mwana wayani?” Davide anati, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese wa ku Betelehemu.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa