Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 2:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Tsono aliyense anagwira mutu wa mnzake namubaya mnzakeyo mʼnthiti ndi mpeni ndipo onse anagwera pansi limodzi. Kotero malo amenewo ku Gibiyoni amatchedwa Helikati Hazurimu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzake, nagwaza ndi lupanga lake m'nthiti mwa mnzake. Chomwecho anagwa limodzi; chifukwa chake malo aja anatchedwa Dera la Mipeni la ku Gibiyoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzake, nagwaza ndi lupanga lake m'nthiti mwa mnzake. Chomwecho anagwa limodzi; chifukwa chake malo aja anatchedwa Dera la Mipeni la ku Gibiyoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono aliyense adagwira mutu wa mnzake nabaya mnzakeyo m'nthitimu ndi lupanga. Choncho onse 24 adafera limodzi. Nchifukwa chake malo amenewo adaŵatchula kuti Helikati-Hazurimu, ndipo ali ku Gibiyoni.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 2:16
7 Mawu Ofanana  

Kenaka Abineri anati kwa Yowabu, “Tiye tibweretse ena mwa anyamata athu kuti amenyane patsogolo pathupa.” Yowabu anayankha, “Chabwino, amenyane.”


Kotero anayimirira ndipo anawawerenga: anyamata khumi ndi awiri a fuko la Benjamini ndi Isi-Boseti mwana wa Sauli ndiponso anyamata khumi ndi awiri a Davide.


Tsiku limeneli nkhondo yake inali yoopsa kwambiri, ndipo Abineri ndi ankhondo a Israeli anagonjetsedwa ndi ankhondo a Davide.


Abineri anayitana Yowabu, “Kodi tipitirize kumenyana mpaka kalekale? Kodi sukuzindikira kuti mathero ake kudzakhala kuwawidwa mitima? Kodi udzawaletsa liti ankhondo ako kuthamangitsa abale awo?”


Ndipo aliyense wa iwo anapha munthu wake. Ataona izi, Aaramu anathawa Aisraeli ali pambuyo pawo kuwapirikitsa. Koma Beni-Hadadi mfumu ya ku Aaramu anathawa atakwera pa kavalo pamodzi ndi ankhondo ena okweranso pa akavalo.


Aliyense mu Yerusalemu anamva zimenezi, kotero anatcha mundawo mʼchiyankhulo chawo kuti Akeledama, kutanthauza, Munda wa Magazi).


Gawo lawo linaphatikiza Helikati, Hali, Beteni, Akisafu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa