Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 19:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Pakati pa mafuko onse a Israeli, anthu amakangana ndipo amati, “Mfumu inatipulumutsa mʼmanja mwa adani anthu. Iye ndi amene anatilanditsa mʼdzanja la Afilisti. Koma tsopano wathawa mʼdziko muno chifukwa cha Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israele analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israele analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndipo onsewo ankangokangana okhaokha. Ankati, “Mfumu Davide adatipulumutsa kwa adani athu, ndipo adatilanditsa kwa Afilisti. Koma tsopano watuluka m'dziko muno, kuthaŵa Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 19:9
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anati kwa akuluakulu ake amene anali mu Yerusalemu. “Bwerani! Tiyeni tithawe, mwina palibe adzapulumuke kwa Abisalomu. Tiyeni tichoke msanga, mwina iye adzabwera msanga ndi kutipitirira, nʼkuwononga ife ndi mzinda wathu ndi lupanga.”


Iwo anatenga Abisalomu ndi kumuponya mʼdzenje lalikulu mʼchipululumo ndipo anawunjikapo miyala ikuluikulu. Nthawiyi Aisraeli onse anathawa kupita ku nyumba zawo.


Ndipo Abisalomu amene ife tinamudzoza kuti atilamulire wafa pa nkhondo. Tsono nʼchifukwa chiyani simukunena kanthu za kubweretsanso mfumu?”


Pamene mfumu inawolokera ku Giligala, Kimuhamu anawoloka naye. Ankhondo onse a Yuda ndi theka la ankhondo a Israeli onse anaperekeza mfumu.


“Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu; Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina. Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.


Choncho Davide anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Yehova waphwanya adani anga ine ndikuona.” Choncho anawatcha malowa Baala Perazimu.


Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa anthu; mwandisandutsa kukhala mtsogoleri wa anthu a mitundu ina. Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.


Choncho ine ndinawawuza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi zokometsera zagolide azivule.’ Choncho iwo anandipatsa golide, ndipo ndinamuponya pa moto ndi kupanga fano la mwana wangʼombeyu.”


Kotero Davide anamupambana Mfilisitiyo pomugenda ndi mwala wa legeni ndi kumupha. Mʼmanja mwa Davide munalibe lupanga.


Sauli anayankha kuti, “Kamuwuzeni Davide kuti, ‘Mfumu sikufuna malowolo a mtundu wina uliwonse koma timakungu ta msonga za mavalo a Afilisti 100 kuti ilipsire adani ake.’ ” Maganizo a Sauli anali akuti Davide aphedwe ndi Afilisti.


Iye anayika moyo wake pa chiswe pamene anapha Mfilisiti uja. Choncho Yehova anachita zazikulu popambanitsa Aisraeli pa nkhondo. Inu munaona zonsezo ndipo munakondwera. Nanga nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa pofuna kupha Davide?”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa