Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 19:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ankhondo analowa mu mzinda mwakachetechete tsiku limenelo ngati momwe amalowera anthu mwamanyazi chifukwa athawa ku nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo tsiku lija anthu analowa m'mzinda kachetechete, monga azemba anthu akuchita manyazi pakuthawa nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo tsiku lija anthu analowa m'mudzi kachetechete, monga azemba anthu akuchita manyazi pakuthawa nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsiku limenelo anthu adaloŵa mu mzinda kachetechete, monga momwe anthu amaloŵera mu mzinda mwamanyazi, akamathaŵa kunkhondo.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 19:3
5 Mawu Ofanana  

Chifukwa chiyani unandinamiza ndi kuthawa mozemba wosandiwuza? Ukanandiwuza, bwezi titatsanzikana mwa chisangalalo ndi kuyimba nyimbo ndi zisekese ndi azeze.


Davide anapita ku Mahanaimu, ndipo Abisalomu anawoloka Yorodani pamodzi ndi ankhondo ena onse a Israeli.


Ndipo kwa asilikali onse chipambano cha tsiku limenelo chinasandulika maliro, chifukwa tsiku limenelo anthu anamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake.


Tsono Barizilai anali wokalamba kwambiri, wa zaka makumi asanu ndi atatu. Iye ndi amene anapereka zinthu kwa mfumu pamene anali ku Mahanaimu pakuti anali wolemera kwambiri.


Mfumu inaphimba nkhope yake ndipo inalira mofuwula, “Iwe mwana wanga Abisalomu! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa