2 Samueli 15:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Pamene mtumiki wanu amakhala ku Gesuri ku Aramu, anachita lonjezo ili: ‘Ngati Yehova adzandibweretsadi ku Yerusalemu, ndidzapembedza Yehovayo mu Hebroni.’ ” Onani mutuwoBuku Lopatulika8 Pakuti mnyamata wanu ndinawinda pakukhala ine ku Gesuri mu Aramu, ndi kuti, Yehova akadzandibwezeranso ndithu ku Yerusalemu, ine ndidzatumikira Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Pakuti mnyamata wanu ndinawinda pakukhala ine ku Gesuri m'Aramu, ndi kuti, Yehova akadzandibwezeranso ndithu ku Yerusalemu, ine ndidzatumikira Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Nthaŵi imene ndinkakhala ku Gesuri ku Aramu, ndidachita lumbiro lakuti, ‘Chauta akadzandibwezeradi ku Yerusalemu, ndidzampembedza ku Hebroni.’ ” Onani mutuwo |
Abisalomu anati kwa Yowabu, “Taona, ine ndinatumiza mawu kwa iwe ndipo ndinati, ‘Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ine ndinabwera kuchokera ku Gesuri? Zikanakhala bwino ndikanakhala komweko!’ Tsono pano ndikufuna kuonana ndi mfumu, ndipo ngati ndili olakwa mfumuyo indiphe.’ ”