Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 15:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo Abisalomu amawonjezera kunena kuti, “Ine ndikanangosankhidwa kukhala woweruza mʼdziko muno bwenzi munthu aliyense amene ali ndi madandawulo kapena milandu akubwera kwa ine ndipo ndikanaonetsetsa kuti chilungamo chachitika.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Abisalomu anatinso, Mwenzi atandiika ine ndikhale woweruza m'dzikomo, kuti munthu yense amene ali ndi mlandu wake kapena chifukwa chake, akadafika kwa ine; ndipo ndikadamchitira zachilungamo!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Abisalomu anatinso, Mwenzi atandiika ine ndikhale woweruza m'dzikomo, kuti munthu yense amene ali ndi mlandu wake kapena chifukwa chake, akadafika kwa ine; ndipo ndikadamchitira zachilungamo!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndipo ankapitirira kunena kuti, “Achikhala adaaika ine, kuti ndikhale woweruza m'dziko muno! Bwenzi munthu aliyense amene ali ndi mlandu, kapena vuto lina lililonse, atabwera kwa ine, ndipo ine ndikadamuweruza molungama munthuyo.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 15:4
7 Mawu Ofanana  

Ndipo nthawi zonse amati munthu akasendera pafupi ndi kumugwandira, Abisalomu amatambalitsa dzanja lake, kumuyimiritsa munthuyo ndi kupsompsona.


Usamadzikuze ukakhala pamaso pa mfumu, ndipo usamakhale pamalo pa anthu apamwamba;


Munthu wina akutamande, koma osati wekha; mlendo akakutamanda, ndiponi koma osati ndi pakamwa pako.


Amawalonjeza ufulu, pomwe iwo eni ndi akapolo a zizolowezi zowononga. Pajatu munthu amakhala kapolo wa chilichonse chimene chikumulamulira.


Anthu a mu mzindawo akanakhala pansi pa ulamuliro wanga, ndikanamuchotsa Abimelekiyu. Ndikanamuwuza Abimeleki kuti, ‘Wonjeza ankhondo ako ndipo ubwere tidzamenyane!’ ”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa