Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 13:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kenaka iye anatenga chiwaya ndipo anamupatsa bulediyo, koma iyeyo anakana. Amnoni anati “Uza aliyense atuluke muno.” Ndipo aliyense anatuluka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo anatenga chiwaya natitulutsa pamaso pake; koma anakana kudya. Ndipo Aminoni anati, Anthu onse atuluke kundisiya ine. Natuluka onse, kumsiya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo anatenga chiwaya natitulutsa pamaso pake; koma anakana kudya. Ndipo Aminoni anati, Anthu onse atuluke kundisiya ine. Natuluka onse, kumsiya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono adatenga chiwaya, nakhuthula makekewo, iye akupenya, koma Aminoniyo adakana kudya. Ndipo Aminoni adati, “Uzani anthu onse achoke.” Choncho anthu onse adachoka.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:9
5 Mawu Ofanana  

Tsono Yosefe sanathenso kuwugwira mtima kuti asalire pamaso pa antchito ake ndipo anafuwula kuti, “Aliyense achoke pamaso panga!” Motero panalibe wina aliyense pamene Yosefe anadziwulula kwa abale ake.


Kenaka Amnoni anati kwa Tamara, “Bweretsa chakudya kuno, ku chipinda changa chogona kuti ndidye chili mʼmanja mwako.” Ndipo Tamara anatenga buledi amene anapanga ndi kubwera naye kwa mlongo wake ku chipinda chake.


Choncho Tamara anapitadi ku nyumba ya mlongo wake Amnoni kumalo kumene ankagona. Anakanda ufa, nawumba buledi Amunoniyo akuona ndipo anaphika bulediyo.


Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere.


Iye mwini anabwerera pamalo a miyala yozokotedwa ku Giligala ndipo anati, “Zikomo mfumu, ine ndili ndi mawu achinsinsi kuti ndikuwuzeni.” Mfumuyo inawuza onse amene amayitumikira kuti akhale chete, ndipo kenaka anawatulutsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa