Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 13:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kotero Amnoni anagona nakhala ngati akudwala. Mfumu itabwera kudzamuona, Amnoni anati kwa iyo, “Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara kuti abwere adzandipangire buledi wapamwamba ineyo ndikuona, kuti ndidye ali mʼmanja mwake.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Chomwecho Aminoni anagona, nadzikokomeza alikudwala; ndipo pamene mfumu inadza kumuona, Aminoni anati kwa mfumuyo, Mulole Tamara mlongo wanga abwere ndi kundipangira timitanda tiwiri pamaso panga, kuti ndikadye cha m'manja mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Chomwecho Aminoni anagona, nadzikokomeza alikudwala; ndipo pamene mfumu inadza kumuona, Aminoni anati kwa mfumuyo, Mulole Tamara mlongo wanga abwere ndi kundipangira timitanda tiwiri pamaso panga, kuti ndikadye cha m'manja mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Choncho Aminoni adagona, nachita ngati wadwala. Mfumu itabwera kudzamuwona, Aminoniyo adauza mfumuyo kuti, “Chonde, mulole mlongo wanga Tamara abwere, kuti adzandiphikire chakudya ine ndikupenya, kuti ndidzadyere m'manja mwake.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:6
4 Mawu Ofanana  

Choncho Abrahamu anafulumira kupita kwa Sara mʼtenti nati, “Tafulumira, tenga mabeseni atatu a ufa wosalala, ukande ndi kupanga buledi.”


Yehonadabu anati, “Pita ukagone ndipo unamizire kudwala. Abambo ako akabwera kudzakuona, udzati kwa iwo, Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara abwere kuti adzandikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho ine ndikumuona ndi kudya chili mʼmanja mwake.”


Davide anatumiza mawu kwa Tamara ku nyumba yaufumu kuti, “Pita ku nyumba ya mlongo wako Amnoni ndipo ukamukonzere chakudya.”


Iye anawawuzanso fanizo lina nati: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza mu ufa wambiri mpaka wonse unafufuma.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa