Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 13:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yehonadabu anati, “Pita ukagone ndipo unamizire kudwala. Abambo ako akabwera kudzakuona, udzati kwa iwo, Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara abwere kuti adzandikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho ine ndikumuona ndi kudya chili mʼmanja mwake.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Ndipo Yonadabu ananena naye, Ugone pa kama wako ndi kudzikokomera ulikudwala; ndipo pamene atate wako akadzakuona unene naye, Mulole mlongo wanga Tamara abwere kundipatsa kudya, nakonzere chakudyacho pamaso panga kuti ndichione ndi kuchidya cha m'manja mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Yonadabu ananena naye, Ugone pa kama wako ndi kudzikokomera ulikudwala; ndipo pamene atate wako akadzakuona unene naye, Mulole mlongo wanga Tamara abwere kundipatsa kudya, nakonzere chakudyacho pamaso panga kuti ndichione ndi kuchidya cha m'manja mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono Yonadabu adamuuza kuti, “Kagone pabedi pako, ndipo uchite ngati wadwala. Bambo wako akafika kuti adzakuwone, umuuze kuti, ‘Mloleni Tamara, mlongo wanga, abwere andikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho konkuno, ine ndikupenya, kuti ndichiwone, ndipo ndidzadyere m'manja mwake.’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:5
8 Mawu Ofanana  

Iye anafunsa Amnoni, “Nʼchifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu, umaoneka wowonda mmawa uliwonse? Bwanji wosandiwuza?” Amnoni anamuyankha kuti, “Ine ndamukonda Tamara, mlongo wa mʼbale wanga Abisalomu.”


Kotero Amnoni anagona nakhala ngati akudwala. Mfumu itabwera kudzamuona, Amnoni anati kwa iyo, “Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara kuti abwere adzandipangire buledi wapamwamba ineyo ndikuona, kuti ndidye ali mʼmanja mwake.”


Ahitofele anayankha kuti, “Mugone ndi azikazi a abambo anu amene awasiya kuti asamalire nyumba yaufumu. Aisraeli onse adzamva kuti mwachitira abambo anu chinthu chonyansa kotheratu ndipo anthu onse amene ali ndi iwe adzalimbikitsidwa.”


Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo, udzapatukana ndi mawu opatsa nzeru.


Tsopano inu pamodzi ndi akuluakulu a Bwalo Lalikulu mupemphe mkulu wa asilikali kuti akubweretsereni Paulo ngati kuti mukufuna kudziwa bwino za mlandu wake. Ife takonzeka kudzamupha asanafike kumeneko.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa