Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 13:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Patapita nthawi, Amnoni mwana wa Davide anakonda Tamara, mlongo wa Abisalomu, mwana wa Davide, amene anali wokongola.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Abisalomu mwana wa Davide, anali ndi mlongo wake wokongola, dzina lake Tamara. Aminoni, mwana wina wa Davide, ankakonda Tamara.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:1
15 Mawu Ofanana  

Yakobo anakonda Rakele ndipo anati, “Ndidzakugwirirani ntchito kwa zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha mwana wanu wamngʼono, Rakele.”


Choncho Yakobo anagwira ntchito zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele. Koma kwa iye zaka zonsezi zinakhala ngati masiku wochepa chifukwa anamukonda Rakele.


Koma Sekemu anamukondadi namwali uja, Dina, mwana wa Yakobo motero kuti anamuyankhula mawu womutonthoza.


ana aamuna a Mulungu anaona kuti ana aakazi a anthuwo anali okongola. Ndipo anakwatira aliyense amene anamusankha.


Tsiku lina cha kumadzulo Davide anadzuka pa bedi lake ndipo ankayenda pamwamba pa nyumba yake. Ali pa dengapo anaona mkazi akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwambiri.


Atatero Amnoni anadana naye kwambiri. Iyeyo anamuda kuposa momwe anamukondera. Amnoni anati, “Dzuka ndipo tuluka!”


Amnoni sankagona tulo mpaka anadwala chifukwa cha Tamara mlongo wakeyo, pakuti iye anali asanagonepo ndi mwamuna ndipo zimaoneka kuti zinali zosatheka kuti achite chilichonse kwa iye.


Abisalomu anali ndi ana aamuna atatu ndi wamkazi mmodzi. Mwana wamkazi dzina lake linali Tamara, ndipo anali mkazi wokongola kwambiri.


Komatu Mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo ndipo kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, analinso ndi akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni, ndi Ahiti.


wachitatu anali Abisalomu, mwana wa Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri; wachinayi anali Adoniya amayi ake anali Hagiti;


Onsewa anali ana a Davide, osawerengera ana a azikazi. Ndipo mlongo wawo anali Tamara.


Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa; koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.


Mu mtima wako usakhumbire kukongola kwake, asakukope ndi zikope zake,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa