Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 12:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 koma wosaukayo analibe chilichonse kupatula kankhosa kamodzi kakakazi kamene anakagula. Iye anakasunga ndipo kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kamadya chakudya chake, kamamwera chikho chake ndipo kamagona mʼmanja mwake. Kanali ngati mwana wamkazi kwa iyeyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kanadyako chakudya chake cha iye yekha, kanamwera m'chikho cha iye yekha, kanagona pa chifukato chake, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wake wamkazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kanadyako chakudya chake cha iye yekha, kanamwera m'chikho cha iye yekha, kanagona pa chifukato chake, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wake wamkazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma wosauka uja analibe nkanthu komwe kupatula kankhosa kakakazi kamodzi, kamene adaagula. Ndipo adakaŵeta kankhosako, mpaka kukula kali ndi iyeyo pamodzi ndi ana ake. Kankadyako chakudya chake cha munthuyo, mpaka kumamwera m'chikho chake. Kankagona pakhundu pake pa munthuyo, ndipo kankakhala ngati mwana wake wamkazi.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 12:3
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anatuma munthu wina kuti akafufuze za iye. Munthuyo anati, “Kodi uyu si Batiseba, mwana wa Eliamu, mkazi wa Uriya Mhiti?”


Munthu wolemerayo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri,


“Ndipo mlendo anafika kwa munthu wolemera uja, koma munthu wolemerayo sanafune kutenga imodzi mwa nkhosa kapena ngʼombe zake kuti akonzere chakudya mlendo amene anafika kwa iye. Mʼmalo mwake anatenga mwana wankhosa wamkazi wa munthu wosauka uja nakonzera chakudya mlendo uja amene anabwera kwa iye.”


Usadalire mnansi; usakhulupirire bwenzi. Usamale zoyankhula zako ngakhale kwa mkazi amene wamukumbatira.


Ngati mʼbale wanu weniweni kapena mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena mnzanu wapamtima akukakamizani mwachinsinsi, nʼkumati, “Tiyeni tipite tikapembedze milungu ina” (milungu imene inuyo kapena makolo anu sanayidziwe,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa