Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 11:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Davide anatumiza Yowabu ndi ankhondo a mfumu pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Aisraeli. Iwo anawononga Aamoni ndi kuzungulira mzinda wa Raba. Koma Davide anatsala ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pa nyengo yophukira mitengo, nthaŵi imene mafumu ankakonda kukamenya nkhondo, Davide adatuma Yowabu ndi atsogoleri ake ndi ankhondo a Aisraele onse. Adaononga Aamoni, nazinga mzinda wa Raba ndi zithando zankhondo. Koma Davide adatsalira ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 11:1
15 Mawu Ofanana  

Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai ndi kulowa mu mzinda. Nkhondo itatha, Yowabu anabwerera ku Yerusalemu.


Zitachitika izi, mneneri wina anabwera kwa mfumu ya Israeli ndipo anati, “Mulimbike ndipo muganize bwino zoti mudzachite, chifukwa chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzakuthiraninso nkhondo.”


Chaka chinacho Beni-Hadadi anasonkhanitsa Aaramu, napita ku Afeki kukamenyana ndi Israeli.


Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Yowabu anatsogolera gulu la ankhondo. Iye anawononga Aamoni, kenaka anapita ku mzinda wa Raba ndipo anawuzungulira, koma Davide anatsala ku Yerusalemu. Yowabu anathira nkhondo mzinda wa Raba ndipo anawuwononga.


Nthawi ya mphukira, mfumu Nebukadinezara inayitanitsa Yehoyakini ndipo inapita naye ku Babuloni, pamodzi ndi ziwiya zamtengowapatali za mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova, ndipo anayika Zedekiya malume wake kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.


Adzandifikitse ndani ku mzinda wotetezedwa? Ndani adzanditsogolera ku Edomu?


Nthawi yokondana ndi nthawi yodana, nthawi ya nkhondo ndi nthawi ya mtendere.


Koma nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondo ku Raba, likulu la Amoni; ndipo malo awo opembedzera milungu yawo adzatenthedwa ndi moto. Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawo kuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,” akutero Yehova.


“Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika! Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba! Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu; thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga, chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo, pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake.


Ulembe chizindikiro pa msewu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wotetezedwa.


Ine ndidzayatsa moto pa makoma a ku Raba umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu. Padzakhala kulira kwakukulu pa tsiku la nkhondoyo, kumenyana kudzakhala kwafumbi ngati mkuntho wa kamvuluvulu.


Pamenepo Yehova adzabwera kudzamenyana ndi mitundu ya anthu imeneyi, ngati mmene amachitira pa nthawi ya nkhondo.


(Ogi, mfumu ya ku Basani, anali yekhayo amene anatsala mwa mtundu wa anthu ataliatali a Chirefai. Bedi lake linali lachitsulo ndipo lalitali kuposa mamita anayi. Mulifupi mwake munali mamita awiri. Bedilo likanalipo ku Raba kwa Aamori).


Nthawi zonse pamene atsogoleri a Afilisti ankatuluka kukamenya nkhondo, Davide ankapambana kuposa nduna zonse za Sauli. Choncho dzina lake linatchuka kwambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa