Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 10:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, anakapeza ankhondo oyenda pansi aganyu okwanira 20,000 kuchokera ku Asiriya wa ku Beti Rehobu ndi Aramu-Zoba, komanso ankhondo 1,000 kwa mfumu Maaka ndiponso ankhondo 22,000 ochokera ku Tobu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono Aamoni atazindikira kuti adziputira mkwiyo wa Davide, adatuma anthu kukalemba ntchito Asiriya a ku Beterehobu ndi a ku Zoba, ankhondo apansi okwanira 20,000. Adalembanso mfumu ya ku Maaka ndi anthu ake okwanira 1,000, ndiponso anthu a ku Tobu okwanira 12,000.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 10:6
24 Mawu Ofanana  

Pamenepo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, “Mwandiputira mavuto, ndi kundiyipitsira dzina pakati pa anthu a mʼdziko lino, Akanaani ndi Aperezi. Ife ndife owerengeka, ndipo atati aphatikizane kudzandithira nkhondo, ndiye kuti ine ndi banja langa tidzawonongeka.”


Atamufotokozera Davide zimenezi, iye anatuma amithenga kukakumana ndi anthuwo chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.”


Davide atamva zimenezi, anatumiza Yowabu ndi gulu lonse la ankhondo amphamvu.


Ahitofele anayankha kuti, “Mugone ndi azikazi a abambo anu amene awasiya kuti asamalire nyumba yaufumu. Aisraeli onse adzamva kuti mwachitira abambo anu chinthu chonyansa kotheratu ndipo anthu onse amene ali ndi iwe adzalimbikitsidwa.”


Elifeleti mwana wa Ahasibai Mmaakati, Eliamu mwana wa Ahitofele Mgiloni,


Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki. Iye anaperekanso zolanda ku nkhondo zochokera kwa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba.


Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.


Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000.


Iye anasonkhanitsa anthu ndipo anali mtsogoleri wa anthu owukira pamene Davide anapha ankhondo a ku Zoba. Anthu owukirawa anapita ku Damasiko, nakakhala kumeneko ndi kuyamba kulamulira.


pakuti Ambuye anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lalikulu la ankhondo, kotero anayamba kuwuzana kuti, “Taonani, mfumu ya ku Israeli yalemba ganyu mafumu a Ahiti ndi a Aigupto kuti adzatithire nkhondo!”


Pamene mafumu anasonkhana pamodzi, pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,


ndipo iwo anati, “Yehova akupenyeni ndi kukuweruzani popeza mwachititsa Farao ndi nduna zake kuti anyansidwe nafe ndipo mwayika lupanga mʼmanja mwawo kuti atiphe.”


usafulumire kupita nacho ku bwalo la milandu nanga udzachita chiyani pa mapeto pake ngati mnansi wako adzakuchititsa manyazi?


Iwowa anapita ku Mizipa kwa Gedaliya. Amene anapitawo ndi awa: Ismaeli mwana wa Netaniya, Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti, ana a Efai a ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa Maaka, iwowo pamodzi ndi anthu awo.


Ngakhale ankhondo aganyu amene ali naye ali ngati ana angʼombe onenepa. Nawonso abwerera mʼmbuyo, nathawa pamodzi. Palibe amene wachirimika. Ndithu, tsiku la tsoka lawafikira; ndiyo nthawi yowalanga.


Yairi, mdzukulu wa Manase, anatenga chigawo chonse cha Arigobu mpaka ku malire a Agesuri ndi Amaakati. Anatcha chigawochi dzina lake, moti mpaka lero Basani amatchedwa Havoti Yairi).


Choncho Yefita anathawa kuchoka kwa abale ake ndi kukakhala mʼdziko la Tobu. Kumeneko anakakopa ndi kusonkhanitsa anthu achabechabe ndipo anatuluka pamodzi kukasakaza zinthu.


Tsono pamene Aamoni ankathira nkhondo Aisraeli, akuluakulu a ku Giliyadi anapita kukamutenga Yefita ku dziko la Tobu.


Panalibe wowapulumutsa chifukwa anali kutali ndi Sidoni ndiponso sanali pa ubale ndi wina aliyense. Mzindawo unali mʼchigwa cha Beti-Rehobu. Anthu a fuko la Adaniwo anawumanganso mzindawo ndi kumakhalamo.


Choncho Aisraeli onse anamva kuti Sauli wakantha mkulu wa ankhondo Wachifilisiti ndi kuti Afilisti anayipidwa nawo Aisraeli. Ndiye anthu anayitanidwa kuti abwere kwa Sauli ku Giligala.


Akisi ankamukhulupirira Davide ndipo ankati mu mtima mwake, “Davide wadzisandutsa munthu woyipa kwambiri pakati pa anthu ake omwe, Aisraeli. Tsono adzakhala mtumiki wanga mpaka kalekale.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa