Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 1:22 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 “Pa magazi a ophedwa, pa mnofu wa amphamvu, uta wa Yonatani sunabwerere, lupanga la Sauli silinabwere chabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

22 Uta wa Yonatani sunabwerere, ndipo lupanga la Saulo silinabwerere chabe, pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Uta wa Yonatani sunabwerera, ndipo lupanga la Saulo silinabwerera chabe, pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 “Uta wa Yonatani sudabwereko chabe osakhetsa magazi a anthu osabayako ankhondo amphamvu. Ndipo lupanga la Saulo silidabwereko chabe osapha anthu.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 1:22
7 Mawu Ofanana  

Taonani, ndidzaukitsa gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina ndi kubwera nalo kuchokera kumpoto kudzamenyana ndi Babuloni. Iwo adzandandalika ankhondo awo ndi kugonjetsa Babuloni. Mivi yawo ili ngati ya ankhondo aluso, yosapita padera.


Mivi yanga idzakhuta magazi awo pamene lupanga langa lidzawononga mnofu: magazi a anthu ophedwa ndi ogwidwa ukapolo, mitu ya atsogoleri a adani.’ ”


Sauli ali mtsogoleri wa Israeli, anachita nkhondo ndi adani awa omuzungulira: Mowabu, Amoni, Edomu mafumu a ku Zoba ndi Afilisti. Kulikonse kumene ankapita ankawagonjetsa.


Anachita nkhondo mwamphamvu ndi kugonjetsa Aamaleki. Choncho anapulumutsa Aisraeli mʼmanja mwa anthu amene ankawalanda zinthu zawo.


Yonatani anavula mkanjo umene anavala ndipo anamupatsa Davide pamodzi ndi zovala za nkhondo, lupanga, uta ndi lamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa