2 Samueli 1:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Pakuti Davide anali atanena kwa iye kuti, “Iwe wadzipha wekha. Pakamwa pako pakunena zokutsutsa wekha, pamene unanena kuti, ‘Ine ndapha wodzozedwa wa Yehova.’ ” Onani mutuwoBuku Lopatulika16 Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; chifukwa pakamwa pako padachita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; chifukwa pakamwa pako padachita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Ndipo Davide adati, “Wadziphetsa wekha, unanena wekha ndi pakamwa pako kuti, ‘Ndidapha wodzozedwa wa Chauta.’ ” Onani mutuwo |
Pamene Davide anamva kuti Nabala wamwalira, iye anati, “Alemekezeke Yehova, walipsira Nabala chipongwe chimene anandichita ndipo anandiletsa ine mtumiki wake kuti ndisachite choyipa. Yehova wabwezera pamutu pa Nabala choyipa chimene iye anachita.” Kenaka Davide anatumiza mawu kwa Abigayeli, kumupempha kuti akhale mkazi wake.