2 Samueli 1:14 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Davide anamufunsanso kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunaope kukweza dzanja lako ndi kupha wodzozedwa wa Yehova?” Onani mutuwoBuku Lopatulika14 Ndipo Davide ananena naye, Bwanji sunaope kusamula dzanja lako kuononga wodzozedwa wa Yehova? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Ndipo Davide ananena naye, Bwanji sunaopa kusamula dzanja lako kuononga wodzozedwa wa Yehova? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Davide adamufunsanso kuti, “Nanga iwe sudachite mantha bwanji kutambalitsa dzanja lako nkupha wodzozedwa wa Chauta?” Onani mutuwo |
Ndipo Samueli anatenga botolo la mafuta nathira mafutawo pa mutu wa Sauli ndipo anapsompsona nati, “Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake, Aisraeli. Iwe udzalamulira anthu a Yehova ndiponso udzawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo owazungulira. Chizindikiro chakuti Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake ndi ichi:
Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.”
Tsono abambo anga, onanitu kansalu ka mkanjo wanu kali mʼdzanja langali! Popeza kuti ndinatha kudula msonga ya mkanjo wanu koma osakuphani, pamenepo mudziwe kuti ine ndilibe maganizo woti ndikuchiteni choyipa kapena kukuwukirani. Sindinakulakwireni ngakhale kuti inu mukufuna moyo wanga kuti mundiphe.