Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 1:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Apo Davide ndi anthu onse amene anali nawo anangʼamba zovala zawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

11 Pomwepo Davide anagwira zovala zake nazing'amba; nateronso anthu onse okhala naye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pomwepo Davide anagwira zovala zake nazing'amba; nateronso anthu onse okhala naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Apo Davide adang'amba zovala zake. Nawonso anthu amene anali naye adachita chimodzimodzi.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 1:11
15 Mawu Ofanana  

Rubeni atabwerera ku chitsime kuja anapeza kuti Yosefe mulibe mʼchitsimemo. Pamenepo iye anangʼamba zovala zake


Pamenepo Yakobo anangʼamba zovala zake, navala chisaka mʼchiwuno mwake. Iye analira maliro a mwana wake masiku ambiri.


Apo onse anangʼamba zovala zawo ndi chisoni. Ndipo anasenzetsa abulu katundu wawo nabwerera ku mzinda konkuja.


Tamara anatsira phulusa pamutu pake ndipo anangʼamba mkanjo wokongoletsedwa umene anavalawo. Iye anagwira manja ake kumutu ndipo anachoka, akulira mokweza pamene amapita.


Mfumu inayimirira, ningʼamba zovala zake ndi kugona pa dothi. Antchito ake onse anayimirira pomwepo atangʼamba zovala zawo.


Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi anthu onse amene anali nawo, “Ngʼambani zovala zanu ndipo muvale ziguduli, muyende mukulira patsogolo pa Abineri.” Mfumu Davide mwini anayenda motsatira chitandacho.


Mfumu ya ku Israeli itangowerenga kalatayo, inangʼamba mkanjo wake ndipo inati, “Kodi ine ndine Mulungu? Kodi ndingathe kupha kapena kupereka moyo? Chifukwa chiyani munthu ameneyu wanditumizira munthu woti ndimuchiritse khate lake? Taonani, iyeyu akungofuna kuti apeze chifukwa choyambanirana nane!”


Pakuti mtima wako walapa, ndipo wadzichepetsa wekha pamaso pa Mulungu pamene unamva zimene Iye ananena motsutsa malo ano ndi anthu ake, ndipo chifukwa iwe unadzichepetsa wekha pamaso pa Ine ndi kungʼamba zovala zako ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, atero Yehova.


Nditamva zimenezi, ndinangʼamba chovala changa ndi mwinjiro wanga ndipo ndinamwetula tsitsi la kumutu kwanga ndi ndevu zanga nʼkukhala pansi ndili wokhumudwa.


Mordekai atamva zonse zimene zinachitika, anangʼamba zovala zake, navala chiguduli ndi kudzola phulusa, ndipo analowa mu mzinda, akulira mokweza ndi mowawidwa mtima.


Mfumu pamodzi ndi omutumikira ake onse amene anamva mawu onsewa sanachite mantha kapena kungʼamba zovala zawo.


Ngʼambani mtima wanu osati zovala zanu. Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu, pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka, ndipo amaleka kubweretsa mavuto.


Koma Barnaba ndi Paulo atamva zimenezi, anangʼamba zovala zawo, nathamangira pakati pa gulu la anthuwo, akufuwula kuti,


Kondwani pamodzi ndi amene akukondwa ndipo lirani ndi amene akulira.


Tsono Yoswa anangʼamba zovala zake nagwada nʼkuweramitsa mutu wake pansi patsogolo pa Bokosi la Yehova. Akuluakulu a Israeli nawonso anadzigwetsa pansi ndipo anakhala pomwepo mpaka madzulo atadziwaza fumbi kumutu kwawo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa