Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 9:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Choncho iwo anadutsa dziko la mapiri a Efereimu ndi dera la Salisa, koma sanawapeze. Anadutsa ku Saalimu koma abuluwo sanawapeze. Kenaka anadutsa dziko la Benjamini, koma osawapezabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efuremu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeze; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu, koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efuremu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeze; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu, koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Iwo adabzola dziko lamapiri la Efuremu ndi la Salisa, koma osaŵapeza. Kenaka adabzola dziko la Salimu, koma kumeneko kunalibenso. Adabzolanso dziko la Benjamini, koma osaŵapezabe.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 9:4
9 Mawu Ofanana  

Mmene ankabwerera kuchokera ku Padanaramu, Yakobo anafika ku Salemu, mzinda wa Sekemu ku Kanaani. Anamanga msasa pamalopo moyangʼanana ndi mzindawo.


Munthu wina wochokera ku Baala-Salisa anabwera atamutengera munthu wa Mulungu malofu a barele makumi awiri opangidwa kuchokera ku zokolola zoyamba kucha, pamodzinso ndi ngala zatsopano za tirigu. Elisa anati kwa munthuyo, “Apatse anthu kuti adye.”


Ndipo Yohane amabatizanso ku Ainoni kufupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri ndipo anthu amabwererabwererabe kudzabatizidwa.


Saalabini, Ayaloni, Itira,


Ndipo Eliezara mwana wa Aaroni anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda ku Gibeya, malo amene anapatsidwa kwa Finehasi mwana wake, mʼdziko lamapiri la Efereimu.


Munthu wina dzina lake Mika wochokera ku dziko la mapiri la Efereimu anawuza amayi ake kuti


Pa nthawi imeneyo ku Israeli kunalibe mfumu. Mlevi wina ankakhala kutali ku dziko lamapiri la Efereimu. Iyeyu anatenga mzikazi wa ku Betelehemu, mʼdziko la Yuda.


Panali munthu wina wochokera ku Ramataimu, Mzofimu wa ku dziko la mapiri la Efereimu. Iyeyu dzina lake anali Elikana ndipo anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu wa fuko la Efereimu.


Tsono abulu a Kisi, abambo ake a Sauli anasowa. Choncho Kisi anati kwa mwana wake Sauli, “Tenga wantchito mmodzi ndipo mupite mukafunefune abuluwo.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa