1 Samueli 9:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Tsono abulu a Kisi, abambo ake a Sauli anasowa. Choncho Kisi anati kwa mwana wake Sauli, “Tenga wantchito mmodzi ndipo mupite mukafunefune abuluwo.” Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Ndipo abulu a Kisi, atate wa Saulo, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Saulo mwana wake, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna abuluwo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo abulu a Kisi, atate wa Saulo, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Saulo mwana wake, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna abuluwo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Tsiku lina Kisi adaona kuti abulu ake asoŵa. Choncho adauza Saulo kuti, “Tenga mmodzi mwa anyamata antchitoŵa, munyamuke, mukaŵafunefune abuluwo.” Onani mutuwo |
Ukachoka pano lero lino, udzakumana ndi amuna awiri kufupi ndi manda a Rakele ku Zeliza mʼmalire mwa dziko la Benjamini ndipo adzakuwuza kuti, ‘Abulu amene munkafunafuna aja apezeka. Ndipo tsopano abambo ako asiya kuganiza za abulu ndipo akudera nkhawa za iwe.’ Iwo akufunsa kuti, ‘Kodi ndidzachita chiyani mmene mwana wanga sakuoneka?’ ”