Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 9:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iyeyu anali ndi mwana dzina lake Sauli, mnyamata wa maonekedwe abwino. Pakati pa Aisraeli onse panalibe wofanana naye. Anali wamtali kotero kuti anthu onse ankamulekeza mʼmapewa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu ena onse anamlekeza m'chifuwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu onse ena anamlekeza m'chifuwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Iyeyo anali ndi mwana dzina lake Saulo, mnyamata wokongola. Pakati pa Aisraele onse panalibenso mnyamata wokongola kupambana iyeyo. Anali wamtali kotero kuti anthu ena onse ankamugwa m'mapewa.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 9:2
10 Mawu Ofanana  

ana aamuna a Mulungu anaona kuti ana aakazi a anthuwo anali okongola. Ndipo anakwatira aliyense amene anamusankha.


Neri anabereka Kisi. Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala.


Yehova akuti, “Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake, kapena munthu wamphamvu kunyadira nyonga zake, kapena munthu wolemera kunyadira chuma chake,


Kumeneko tinaona Anefili (ana a Aanaki ochokera kwa Nefili). Ifeyo timangodziona ngati ziwala mʼmaso mwawo, ndipo kwa iwo timaonekadi motero ndithu.”


Anasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja. Pomaliza anasonkhanitsa banja la Matiri mmodzimmodzi ndipo Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa. Koma atamufunafuna, sanamupeze.


Koma Yehova anati kwa Samueli, “Usaone maonekedwe ake kapena msinkhu wake, pakuti ndamukana iyeyu. Yehova sapenya zimene munthu amapenya. Anthu amapenya zakunja, koma Mulungu amapenya za mu mtima.”


Tsono munthu wina wamphamvu, dzina lake Goliati wochokera ku Gati anatuluka ku misasa ya Afilisti. Msinkhu wake unali pafupipafupi mamita atatu.


Tsono abulu a Kisi, abambo ake a Sauli anasowa. Choncho Kisi anati kwa mwana wake Sauli, “Tenga wantchito mmodzi ndipo mupite mukafunefune abuluwo.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa