Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 5:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma atafika nalo ku Gati, Yehova analanga mzindawo, ndipo anthu anachita mantha aakulu. Iye anazunza anthu a mu mzindawo, ana ndi akulu omwe, ndi zithupsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang'ono; ndi mafundo anawabuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mudziwo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mudziwo, akulu ndi ang'ono; ndi mafundo anawabuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma atafika nalo ku Gati, Chauta adauvuta mzindawo, ndipo anthu adachita mantha kwambiri. Choncho anthu amumzindamo adazunzika kwabasi, ana ndi akulu omwe, kotero kuti mafundo ankaŵatuluka anthu onsewo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 5:9
11 Mawu Ofanana  

Iye anathamangitsa adani ake; anawachititsa manyazi ku nthawi zonse.


Lidzakhala ngati tsiku limene munthu pothawa mkango amakumana ndi chimbalangondo, ngati pamene munthu walowa mʼnyumba, natsamira dzanja lake pa khoma ndipo njoka nʼkuluma.


Dzanja la Yehova linatsutsana nawo mpaka wonse anathera ku msasa.


Koma mukapanda kumvera Yehova ndi kumupandukira, ndiye adzakulangani pamodzi ndi mfumu yanu yomwe.


Choncho anatumiza Bokosi la Mulungu ku Ekroni. Koma Bokosi la Mulungu lija litangofika ku Ekroni, anthu a ku Ekroni analira kuti, “Abwera nalo Bokosi la Mulungu wa Israeli kwa ife kuti atiphe pamodzi ndi anthu athu.”


Kotero iwo anayitana atsogoleri onse a Afilisti kuti asonkhane ndipo anati, “Chotsani Bokosi la Mulungu wa Israeli, libwerere ku malo ake. Tikapanda kutero lidzatipha ife ndi anthu athu.” Pakuti mu mzinda monse munali mantha aakulu kwambiri ndipo Mulungu ankawalanga kwambiri anthu a kumeneko.


Yehova analanga koopsa anthu a ku Asidodi. Yehova anawawononga ndi kuwazunza ndi zithupsa Asidoniwa pamodzi ndi anthu a madera ozungulira.


Tsono anayika Bokosi la Yehova pa galeta pamodzi ndi bokosi limene munali makoswe agolide ndi zifanizo zawo za zithupsa.


Kotero Afilisti anagonjetsedwa ndipo sanadzalowenso mʼdziko la Israeli. Yehova analimbana ndi Afilisti masiku onse a Samueli.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa