1 Samueli 5:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Kenaka anatenga Bokosi la Chipanganolo nabwera nalo ku nyumba ya Dagoni ndi kuliyika pambali pa Dagoni. Onani mutuwoBuku Lopatulika2 Ndipo Afilistiwo anatenga likasa la Mulungu, nafika nalo kunyumba ya Dagoni, naliika pafupi ndi Dagoni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo Afilistiwo anatenga likasa la Mulungu, nafika nalo kunyumba ya Dagoni, naliika pafupi ndi Dagoni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Tsono adatenga Bokosilo nakaliika m'nyumba ya Dagoni, mulungu wao, pambali pa Dagoniyo. Onani mutuwo |
Mʼmalo mwake, mwadzikweza nokha kutsutsana ndi Ambuye wakumwamba. Inu mwatenga ziwiya za mʼNyumba mwake, ndipo inu ndi akalonga anu, akazi anu ndi azikazi anu mwamwera vinyo mu zimenezi. Inu munatamanda milungu yasiliva ndi golide, yamkuwa, chitsulo, mtengo ndi mwala, imene singaone kapena kumva kapena kuzindikira. Koma simunamupatse ulemu Mulungu amene asunga mʼmanja mwake moyo wanu ndi njira zanu zonse.