Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 3:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Yehova anayitananso, “Samueli!” Ndipo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli nati, “Ndabwera popeza ndamva mukundiyitana.” Eli nati, “Mwana wanga, ine sindinakuyitane, bwerera kagone.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samuele. Ndipo Samuele anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitane, mwana wanga; kagone.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samuele. Ndipo Samuele anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitana, mwana wanga; kagone.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Pambuyo pake Chauta adamuitananso kuti, “Samuele!” Pompo Samuele adadzuka napita kwa Eli nakamuuza kuti, “Ndabwera, ndamva ndithu kuitana.” Koma Eli adati, “Sindidakuitane mwana wanga, kagone.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 3:6
6 Mawu Ofanana  

Pomwazamwaza maso Yosefe anaona Benjamini, mʼbale wake weniweni wa bere limodzi, ndipo anafunsa, “Kodi uyu ndiye mʼbale wanu wamngʼono kwambiri amene munkandiwuza uja?” Kenaka anati, “Ambuye akukomere mtima mwana wanga.”


Ahimaazi mwana wa Zadoki ananenanso kwa Yowabu kuti, “Zivute zitani, chonde mundilole kuti ndipite pambuyo pa Mkusiyo.” Koma Yowabu anayankha kuti, “Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukufuna kupita? Ulibe nkhani yoti ukalandire nayo mphotho.”


Amuna ena anabwera ndi munthu wakufa ziwalo kwa Iye atamugoneka pa mphasa. Yesu ataona chikhulupiriro chawo anati kwa wakufa ziwaloyo, “Limba mtima mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”


Ndipo iyeyo anathamangira kwa Eli ndipo anati, “Ndabwera ndamva kuyitana.” Koma Eli anati, “Ine sindinakuyitane, bwerera kagone.” Ndipo iye anapita kukagona.


Nthawiyi nʼkuti Samueli asanadziwe Yehova ndipo Mawu a Yehova nʼkuti asanawululidwe kwa iye.


Munthuyo anamuwuza Eli kuti, “Ine ndabwera kuchokera ku nkhondo, ndathawako lero lomwe lino.” Eli anafunsa, “Nanga nkhondo yayenda bwanji mwana wanga?”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa